CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 10-13
Yehova ni Wokhulupilika
Yehova angasankhe kuthetsa mayeselo. Komabe, nthawi zambili amapeleka “njila yopulumukila” mwa kutipatsa zimene tifunikila kuti tipilile mayeselowo.
Angatithandize kukhala na maganizo oyenelela, kutilimbikitsa, na kutitonthoza kupitila m’Mawu ake, mzimu woyela, komanso cakudya cauzimu cimene amatipatsa.—Mat. 24:45; Yoh. 14:16; Aroma 15:4
Angatitsogolele na mzimu woyela, umene ungatithandize kukumbukila mfundo komanso nkhani za m’Baibo kuti tizindikile njila yoyenela kutsatila.—Yoh. 14:26
Iye angaseŵenzetse angelo kuti atithandize.—Aheb. 1:14
Angatithandize kupitila mwa olambila anzathu.—Akol. 4:11