CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AFILIPI 1-4
“Musamade Nkhawa ndi Kanthu Kalikonse”
4:6, 7
Pemphelo ndiye mankhwala a nkhawa
Ngati tipemphela tili na cikhulupililo, Yehova adzatipatsa mtendele umene “umaposa kuganiza mozama kulikonse”
Ngakhale tithedwe nzelu na mavuto amene takumana nawo, Yehova angatithandize kuwapilila. Angatithandize m’njila imene sitinali kuyembekezela.—1 Akor. 10:13