July 1-7
AKOLOSE 1-4
Nyimbo 56 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Vulani Umunthu Wakale, Muvale Watsopano”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Akolose.]
Akol. 3:5-9—“Vulani umunthu wakale” (w11 3/15 10 ¶12-13)
Akol. 3:10-14—“Muvale umunthu watsopano” (w13 9/1 21 ¶18-19)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Akol. 1:13, 14—Kodi “ufumu wa Mwana wake wokondedwa” n’ciani? (it-2 169 ¶3-5)
Akol. 2:8—Kodi “mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli” n’ciani? (w08 8/15 28 ¶8)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Akol. 1:1-20 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa, ndiyeno kambilanani phunzilo 7 m’bulosha ya Kuphunzitsa.
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) 04 5/1 19-20 ¶3-7—Mutu: Kodi Paulo ‘analimbikitsidwa’ bwanji na Akhristu ena? (Akol. 4:11) (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lipoti la Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa la 2018: (15 min.) Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno kambilanani mafunso aya: N’cifukwa ciani maulendo akhala mbali yofunika pa zocitika za m’gulu lathu? Kodi Dipatimenti Yokonza Maulendo ku likulu lathu, limacita ciani kuti pasawonongeke ndalama zambili za Ufumu? Kodi ofalitsa angacite ciani kuti acepetseko ndalama zimene zimatayika pa maulendo okhudza gulu lathu? Kodi Dipatimenti Yokonza Maulendo ku likulu lathu, ikuthandiza bwanji abale na alongo opita ku misonkhano ya maiko ya 2019?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 73
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 102 na Pemphelo