UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kudzipeleka Kwa Mulungu na Kucita Maseŵela Olimbitsa Thupi
Kodi kucita maseŵela olimbitsa thupi n’kopindulitsa? Inde, koma n’kopindulitsa pang’ono tikakuyelekezela na kucita zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wathu na Yehova. (1 Tim. 4:8) Conco, m’poyenela kuti Akhristu aziona maseŵela olimbitsa thupi moyenelela.
TAMBITSANI VIDIYO YA TUKADOLI YAKUTI ZIMENE MUFUNIKA KUDZIŴA ZOKHUDZA MASEŴELA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
1. Ni maluso ati amene tingaphunzile pocita maseŵela?
2. Ni zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize kudziŵa ngati maseŵela ena ake ali bwino kwa ise kapena ayi?
3. Kodi lemba la Salimo 11:5 lingatithandize bwanji posankha mtundu wa maseŵela amene tingaonelele kapena kucita?
4. Kodi malemba a Afilipi 2:3 na Miyambo 16:18, angatithandize bwanji pamene ticita maseŵela athu?
5. Kodi lemba la Afilipi 1:10, lingatithandize bwanji ngati timathela nthawi yaitali kwambili kutamba kapena kucita maseŵela?