UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mungafotokoze Cikhulupililo Canu?
Ngati munthu wakufunsani cifukwa cake mumakhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse, mungamuyankhe bwanji? Kuti mumuyankhe mwa cidalilo, mufunika kucita zinthu ziŵili: Coyamba , mufunika kupeza umboni wokukhutilitsani inumwini wakuti zinthu zinacita kulengedwa. (Aroma 12:1, 2) Caciŵili, mufunika kudziŵa mmene mungafotokozele munthu wina zimene mumakhulupilila.—Miy. 15:28.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI DOKOTA WOONA ZA MAFUPA AFOTOKOZA CIKHULUPILILO CAKE, KOMANSO YAKUTI KATSWILI WA ZA NYAMA AFOTOKOZA CIKHULUPILILO CAKE, KUTI MUONE ZIFUKWA ZIMENE ENA ALI NAZO ZOKHULUPILILA KUTI ZINTHU ZINACITA KULENGEDWA, NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani Irène Hof Laurenceau amakhulupilila kuti zinthu zinacita kulengedwa m’malo mokhulupilila za cisanduliko?
N’cifukwa ciani Yaroslav Dovhanych amakhulupilila kuti zinthu zinacita kulengedwa m’malo mokhulupilila za cisanduliko?
Kodi mungamufotokozele bwanji munthu wina cifukwa cake mumakhulupilila kuti zinthu zinacita kulengedwa?
Ni zofalitsa ziti za m’gulu la Yehova zimene muli nazo m’citundu canu, zimene zingakuthandizeni imwe na anthu ena kupeza maumboni oonetsa kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse?