February 24–March 1
GENESIS 20-21
Nyimbo 108 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Nthawi Zonse Amakwanilitsa Malonjezo Ake”: (10 min.)
Gen. 21:1-3—Sara anakhala na pakati ndipo anabeleka mwana wamwamuna (wp17.5 14-15)
Gen. 21:5-7—Yehova anacititsa zinthu zosatheka kukhala zotheka
Gen. 21:10-12, 14—Abulahamu na Sara anali na cikhulupililo colimba pa lonjezo la Yehova lokamba za Isaki
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 20:12—Kodi Sara anali mlongosi wake wa Abulahamu m’njila yanji? (wp17.3 12, ftn.)
Gen. 21:33—Kodi Abulahamu ‘anaitanila motani pa dzina la Yehova’? (w89 7/1 20 ¶9)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 20:1-18 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Kenako funsani omvetsela mafunso aya: Kodi wofalitsa walifotokoza bwanji lemba kuti lipindulitse mwininyumba? N’cifukwa ciani ici ni citsanzo cabwino pa nkhani yothandiza munthu amene waonetsa cidwi?
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 4)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 35 ¶19-20 (th phunzilo 3)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lipoti la Caka Cautumiki: (15 min.) Nkhani ya mkulu. Pambuyo poŵelenga cilengezo cocokela ku ofesi yanthambi cokhudza lipoti la caka cautumiki, funsani mafunso ofalitsa amene munawakonzekeletsa pasadakhale, kuti asimbe zokumana nazo zolimbikitsa za mu ulaliki m’caka capita ca utumiki.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 105
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 119 na Pemphelo