LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 June tsa. 5
  • Kodi Mungaphunzile Ciani kwa Akhristu Amene ni Aciyambakale?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mungaphunzile Ciani kwa Akhristu Amene ni Aciyambakale?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Phunzilani kwa Ofalitsa Amene Atumikila Zaka Zambili
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Musaleke Kulambila Yehova pa Nthawi ya Ciletso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Yehova Akutsogolela Gulu Lake
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Anagonjetsa Tsankho
    Galamuka!—2020
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 June tsa. 5
Mlongo wacicepele wagwila dzanja la mlongo wacikulile.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mungaphunzile Ciani kwa Akhristu Amene ni Aciyambakale?

M’mipingo yathu tili na abale na alongo amene atumikila Yehova kwa zaka zambili. Tingaphunzile zambili pa citsanzo cawo cosagwedezeka codalila Yehova. Tingawafunse zokhudza mbili ya gulu la Yehova na mavuto amene akumana nawo, komanso mmene awagonjetsela mwa thandizo la Yehova. Tingaitanilekonso mmodzi wa abale okondedwa amenewa pa Kulambila kwa Pabanja kuti atifotokozeleko zinthu zokondweletsa zimene apeza pa utumiki wawo.

Ngati ndimwe ciyambakale, khalani womasuka kufotokozela Akhristu acicepele za cikhulupililo canu. Yakobo na Yosefe anauzako ana awo zinthu zimene Yehova anawacitila. (Gen. 48:21, 22; 50:24, 25) Pambuyo pake, Yehova analamula mitu ya mabanja kuphunzitsa ana awo zinthu zazikulu zimene iye anawacitila. (Deut. 4:9, 10; Sal. 78:4-7) Masiku ano, makolo komanso anthu ena mu mpingo angamafotokozeleko acicepele za nchito zodabwitsa zimene aona Yehova akukwanilitsa kupitila m’gulu lake.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KUSUNGA MGWILIZANO PA NTHAWI YA CILETSO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Ofesi Yanthambi ya ku Austria inathandiza bwanji abale athu a kumaiko ena kumene nchito yathu inali yoletsedwa?

  • Kodi abale a m’maiko amenewa anasunga bwanji cikhulupililo cawo cili colimba?

  • N’cifukwa ciani ofalitsa ambili ku Romania anasiya kugwilizana na gulu la Yehova? Nanga anayambanso bwanji kugwilizana nayo?

  • Kodi zocitika zimenezi zilimbitsa bwanji cikhulupililo canu?

Zithunzi: Zocitika za m’vidiyo yakuti ‘Kusunga Mgwilizano Pa Nthawi Ya Ciletso.’ 1. Mapu yoonetsa maiko amene nchito yathu inali yoletsedwa ku Eastern Europe. 2. Mashini a mimeograph. 3. Abale a ku Romania akukumbatilana.

Pezani cuma ca kuuzimu kucokela kwa Akhristu amene ni aciyambakale!

Bwanji ngati ofalitsa ambili mu mpingo mwanu anabatizika m’zaka zaposacedwa? Mungapeze zitsanzo za Mboni zakale pa jw.org mu laibulale pambali yakuti “Mavidiyo” kapena mu Watch Tower Publications Index pa mutu wakuti “Mbili ya Moyo wa Mboni za Yehova.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani