August 10-16
EKSODO 15-16
Nyimbo 149 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tamandani Yehova mwa Kuimba Nyimbo”: (10 min.)
Eks. 15:1, 2—Mose na amuna aciisiraeli anaimba nyimbo zotamanda Yehova (w95 10/15 11 ¶11)
Eks. 15:11, 18—Yehova ni woyenela citamando cathu (w95 10/15 11-12 ¶15-16)
Eks. 15:20, 21—Miriamu na akazi aciisiraeli anaimbila Yehova zitamando (it-2 454 ¶1; 698)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 16:13—Pamene Aisiraeli anali m’cipululu, kodi cingakhale cifukwa citi cimene Yehova anasankhila kuwapatsa zinzili? (w11 9/1 14)
Eks. 16:32-34—Kodi mtsuko wa mana anali kuusungila kuti? (w06 1/15 31)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 16:1-18 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela: Kodi mlongo Linda waseŵenzetsa bwanji mafunso mwaluso? Nanga walifotokoza bwanji lemba momveka bwino?
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo, ndiyeno gaŵilani cofalitsa ca mu Thuboksi Yathu. (th phunzilo 3)
Ulendo Woyamba: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno chulani na kukambilana vidiyo yakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? (koma musaitambitse) (th phunzilo 9)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Tamandani Yehova Monga Mpainiya”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Alongo Atatu a Pacibale ku Mongolia. Funsani m’bale kapena mlongo wa mumpingo mwanu, amene akutumikila monga mpainiya, kapena amene anacitapo utumikiwu kumbuyoku. Funsani mafunso otsatilawa: Kodi munali na zopinga zotani pa utumiki wanu wa upainiya? Nanga ni madalitso otani amene mwapeza?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 127,na bokosi yakuti “Munda wa Magazi”
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 16 na Pemphelo