August 17-23
EKSODO 17-18
Nyimbo 79 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Amuna Odzicepetsa Amaphunzitsa Ena Nchito na Kuwagaŵila Maudindo”: (10 min.)
Eks. 18:17, 18—Yetero anaona kuti Mose anali na nchito yaikulu (w13 2/1 6)
Eks. 18:21, 22—Yetero analimbikitsa Mose kuti agaŵileko nchito zina kwa amuna oyenelela (w03 11/1 6 ¶1)
Eks. 18:24, 25—Mose anaseŵenzetsa malangizo a Yetero (w02 5/15 25 ¶5)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 17:11-13—Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Aroni na Hura amene anacitapo kanthu mwamsanga kuti athandize Mose? (w16.09 6 ¶14)
Eks. 17:14—N’cifukwa ciani zimene Mose analemba zinakhala mbali ya mabuku ouzilidwa a Baibo? (it-1 406)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 17:1-16 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela: Kodi tingaphunzilepo ciani tikaona mmene mlongo Linda wayankhila Jamie pankhani ya anthu akufa? Kodi mlongo Linda wamveketsa motani mfundo yofunika ya pa mavesiwo?
Ulendo Wobwelelako: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 12)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, na kuyambitsa Phunzilo la Baibo m’phunzilo 6. (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (15 min.)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 128
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 14 na Pemphelo