August 24-30
EKSODO 19-20
Nyimbo 88 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mfundo za Malamulo Khumi Zotithandiza”: (10 min.)
Eks. 20:3-7—Kulemekeza Yehova na kudzipeleka kwa iye yekha (w89 11/15 6 ¶1)
Eks. 20:8-11—Kuika zinthu zauzimu patsogolo mu umoyo wathu
Eks. 20:12-17—Kulemekeza anthu ena (w89 11/15 6 ¶2-3)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 19:5, 6—N’cifukwa ciani Aisiraeli anataya mwayi wokhala “ufumu wa ansembe”? (it-2 687 ¶1-2)
Eks. 20:4, 5—Kodi zikutanthauza ciani kuti Yehova ‘amalanga ana cifukwa ca atate awo’? (w04 3/15 27 ¶1)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 19:1-19 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani kakhadi kongenela pa webusaiti yathu. (th phunzilo 1)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo.. Ndiyeno gaŵilani cofalitsa ca mu Thuboksi Yathu. (th phunzilo 15)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 68 ¶17-19 (th phunzilo 8)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Ningacite Ciani kuti Makolo Anga Anipatse Ufulu Wowonjezeleka?: (6 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo ya tukadoli. Ndiyeno funsani acicepele m’gulu: Kodi mungacite ciani kuti makolo anu azikudalilani? Kodi n’ciani cimene mufunika kucita mukalakwitsa zinazake? N’cifukwa ciani kulemekeza makolo n’kofunika kuti akupatseni ufulu wowonjezeleka?
Lemekezani Makolo Anu Acikulile: (9 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela: Kodi pangakhale zopinga zotani pamene makolo akukalamba? N’cifukwa ciani banja lifunika kukambilana bwino posankha mtundu wacithandizo cimene afuna kupatsa makolo awo? Kodi ana amaonetsa bwanji kuti amalemekeza makolo awo pamene aŵasamalila?
Phunzilo la Baibo la Mpingo:(30 min.) jy mutu 129, na bokosi yakuti “Kukwapula”
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 13 na Pemphelo