September 7-13
EKSODO 23-24
Nyimbo 34 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Usatsatile Khamu la Anthu”: (10 min.)
Eks. 23:1—“Usafalitse nkhani yabodza” (w18.08 4 ¶7-8)
Eks. 23:2—Usalole khamu la anthu kukunyengelela kucita zoipa (it-1 11 ¶3)
Eks. 23:3—Usakondele anthu ena (it-1 343 ¶5)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 23:9—Kodi Yehova anawauza ciani Aisiraeli pankhani yocitila cifundo alendo? (w16.10 9 ¶4)
Eks. 23:20, 21—Kodi pali umboni wotani wotsimikizila kuti mngelo amene akuchulidwa palembali ni Mikayeli? (it-2 393)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 23:1-19 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela: Kodi wofalitsayo wacita ciani kuti asasokoneze ulaliki pamene mwininyumba wapeleka yankho yolakwika? Akanafuna, kodi wofalitsayo akanacita ciani kuti agaŵile Nsanja ya Mlonda No. 3 2020?
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Kenako chulani na kukambilana vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? (koma musaitambitse) (th phunzilo 1)
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w16.05 30-31—Mutu: Kodi Mkhristu Angadziŵe Bwanji Ngati N’zoyenela Kupeleka Ndalama Yoyamikila Wogwila Nchito wa Boma? ( th phunzilo 14)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Pewani Kufalitsa Nkhani Zabodza”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yatukadoli yakuti Kodi Ningakanize Bwanji Mijedo?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) jy mutu 131
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 145 na Pemphelo