September 14-20
EKSODO 25-26
Nyimbo 18 na Pemphelo
Mau Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Cimene Cinali Cofunika Kwambili m’Cihema”: (10 min.)
Eks. 25:9—Yehova anapeleka pulani ya mopangila likasa la cipangano (it-1 165)
Eks. 25:21—Likasa linali malo opatulika osungilamo miyala iŵili ya Malamulo Khumi (it-1 166 ¶2)
Eks. 25:22—Likasa linali kuimila kukhalapo kwa Mulungu (it-1 166 ¶3)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 25:20—Kodi zikuoneka kuti n’cifukwa ciani akelubi anaikidwa mwa njila imeneyi pa civundikilo ca Likasa? (it-1 432 ¶1)
Eks. 25:30—Kodi mkate wacionetselo unali ciani? (it-2 936)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 25:23-40 ( th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela: Kodi wofalitsayo waonetsa bwanji mzimu waubwenzi na cifundo? Nanga akanafuna, akanagaŵila bwanji cofalitsa ca mu Thuboksi Yathu?
Ulendo Wobwelelako: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 8)
Ulendo Wobwelelako: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani cofalitsa ca mu Thuboksi Yathu. (th phunzilo 11)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zimene Gulu Likukwanilitsa: (5 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa ya September.
Zofunikila za Mpingo: (10 min.)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) jy mutu 132, na bokosi yakuti “M’pachikeni”
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 20 na Pemphelo