October 26–November 1
EKSODO 37-38
Nyimbo 43 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Maguwa Ansembe a pa Cihema Komanso Nchito Yawo pa Kulambila Koona”: (10 min.)
Eks. 37:25—Guwa la nsembe zofukiza linali kukhala m’Malo Oyela (it-1 82 ¶3)
Eks. 37:29—Zofukiza zopatulika zinali zosakanizidwa mwaluso (it-1 1195)
Eks. 38:1—Guwa la nsembe zopseleza linali kukhala m’bwalo la cihema (it-1 82 ¶1)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 37:1, 10, 25—N’cifukwa ciani mthethe unali mtengo wabwino kwambili wopangila zinthu za pa cihema? (it-1 36)
Eks. 38:8—Kodi magalasi odziyang’anila akale anali osiyana bwanji ndi a masiku ano? (w15 4/1 15 ¶4)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 37:1-24 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 3)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani magazini yatsopano imene iyankha funso limene mwininyumba wafunsa. (th phunzilo 12)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 199 ¶8-9 (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (5 min.)
“Kampeni Yapadela Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu November”: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani na kukambilana vidiyo ya ulendo woyamba ya mwezi wa November.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) jy mutu 138
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 22 na Pemphelo