December 7-13
LEVITIKO 10-11
Nyimbo 32 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Cikondi pa Yehova Ciyenela Kukhala Cacikulu Kuposa Cikondi pa Acibale”: (10 min.)
Lev. 10:1, 2—Yehova anapha Nadabu na Abihu cifukwa copeleka zofukiza pa moto wosaloledwa na Yehova (it-1 1174)
Lev. 10:4, 5—Mitembo yawo anaicotsa mu msasa
Lev. 10:6, 7—Yehova analamula Aroni na ŵana ŵake otsala kuti asacite zinthu zoonetsa cisoni (w11 7/15 31 ¶16)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu (10 min.)
Lev. 10:8-11—Tiphunzilapo ciani pa mavesi amenewa? (w14 11/15 17 ¶18)
Lev. 11:8—Kodi Akhristu sayenela kudya zakudya zimene zinali zoletsedwa m’Cilamulo ca Mose? (it-1 111 ¶5)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Lev. 10:1-15 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso awa: Kodi Tony wacita bwanji pamene mwininyumba anafuna kuimitsa makambilano? Kodi mungakambilane bwanji na munthu lemba la Salimo 1:1, 2?
Ulendo Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Patsani mwininyumba kapepa koitanila kumisonkhano, ndiyeno chulani za vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? (koma musaitambitse) (th phunzilo 20)
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w11 2/15 12—Mutu: N’ciani Cinamukhazika Mtima Pansi Mose Atakwiyila Eleazara na Itamara? (th phunzilo 12)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Timaonetsa Cikondi Ngati Ticita Zinthu Mogwilizana na Cilango ca Yehova”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khalanibe Okhulupilika na Mtima Wonse.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) lfb phunzilo 7, 8
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 39 na Pemphelo