October 4-10
YOSWA 8-9
Nyimbo 127 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Zimene Tingaphunzile pa Nkhani ya Agibeoni”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Yos. 8:29—N’cifukwa ciani mfumu ya Ai inapacikidwa pa mtengo? (it-1 1030)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Yos. 8:28–9:2 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki, koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 2)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Yambani na makambilano acitsanzo. Gaŵilani mwininyumba kapepala koitanila anthu ku misonkhano. Ndiyeno chulani za vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? (koma musaionetse). (th phunzilo 11)
Nkhani: (Mph. 5) it-1 520; 525 ¶1—Mutu: Tiphunzilapo Ciani pa Pangano Limene Yoswa Anacita na Agibeoni? (th phunzilo 13)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Onetsani Kudzicepetsa (1 Pet. 5:5): (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyo imeneyi. Kenako, funsani omvetsela mafunso awa: Kodi Petulo na Yohane anatsatila bwanji malangizo amene Yesu anawapatsa okhudza Pasika? Pa usiku woti maŵa aphedwa, kodi Yesu anaphunzitsa mfundo yanji pa nkhani ya kudzicepetsa? Tidziŵa bwanji kuti Petulo na Yohane anaphunzilapo kanthu pa zimene Yesu anaphunzitsa? Kodi tingaonetse kudzicepetsa m’njila ziti?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 58
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 40 na Pemphelo