April 4-10
1 SAMUELI 20-22
Nyimbo 90 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mmene Mungakhalile Bwenzi Labwino”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
1 Sam. 21:12, 13—Kodi tingaphunzilepo ciani pa zimene Davide anacita? (w05 3/15 24 ¶4)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 1 Sam. 22:1-11 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 2) Citani ulendo wobwelelako kwa munthu amene anaonetsa cidwi ndipo analandila ciitanilo ca ku Cikumbutso. (th phunzilo 6)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 5) Nkhani ya Cikumbutso ikatha, yambitsani makambilano na munthu amene munamuitanila ku Cikumbutso. Yankhani funso limene wafunsa lokhudza pulogilamuyo. (th phunzilo 12)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 04 mfundo 3 (th phunzilo 20)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Mabwenzi Anu a pa Intaneti Ni Otani?”: (Mph. 10) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti.
Landilani Alendo: (Mph. 5) Nkhani yokambidwa na woyang’anila utumiki yozikidwa pa nkhani ya m’kabuku ka Umoyo na Utumiki ka March 2016. Fotokozani zimene mpingo wacitapo kale pa nchito yomemeza anthu ku Cikumbutso. Chulani za ndandanda ya kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso, imene ili pa masamba 10 na 11, ndipo limbikitsani onse kukonzekeletsa mitima yawo kaamba ka Cikumbutso. (Ezara 7:10) Kumbutsani mpingo za makonzedwe amene apangidwa okhudza kupezeka pa Cikumbutso kapena kuonelela pulogilamu ya Cikumbutso.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 84
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 118 na Pemphelo