August 15-21
1 MAFUMU 5-6
Nyimbo 122 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anagwila Nchito Molimbika Cifukwa Cokonda Yehova”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
1 Maf. 6:1—Kodi vesi imeneyi itiuza ciyani za Baibo? (g 5/12 17, bokosi)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 1 Maf. 5:1-12 (th phunzilo 12)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Yambitsani makambilano poseŵenzetsa mfundo za pa cikuto cakumbuyo ca kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Panganani naye kuti ulendo wotsatila mukayankhe funso lalikulu m’phunzilo 01, limenenso ni mutu wa phunzilolo. (th phunzilo 11)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Kambilanani na munthu amene analandila kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! na kumuonetsa mmene phunzilo la Baibo limacitikila. (th phunzilo 2)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 06 mfundo 5 (th phunzilo 9)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kuona Dzanja la Yehova Pomanga Nyumba za Ufumu: (Mph. 15) Onetsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvela mafunso awa: Kodi ni zocitika ziti zimene zinapeleka umboni wakuti Yehova anali kudalitsa nchito yomanga Nyumba za Ufumu ku Micronesia? Kodi mzimu woyela umathandiza bwanji pa nchito yomanga malo olambilila? Kodi inu munaonako bwanji dalitso la Yehova pa nchito zamamangidwe za m’gulu lathu zimene munagwilako?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 16
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 20 na Pemphelo