LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 January masa. 14-15
  • February 26–March 3

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • February 26–March 3
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 January masa. 14-15

FEBRUARY 26–MARCH 3

MASALIMO 11-15

Nyimbo 139 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Yelekezani Kuti Muli m’Dziko Latsopano la Mulungu Komanso la Mtendele

(Mph. 10)

Kusamvela malamulo n’kumene kumabweletsa ciwawa cimene tikuona masiku ano (Sal. 11:​2, 3; w06 5/15 18 ¶3)

Timakhulupilila kuti posacedwa Yehova adzathetsa ciwawa (Sal. 11:5; wp16.4 11)

Kusinkhasinkha za lonjezo lakuti Yehova adzatipulumutsa kumatithandiza kuyembekezela dziko latsopano moleza mtima (Sal. 13:​5, 6; w17.08 6 ¶15)

Mopanda mantha mtsikana wagona m’munsi mwa mtengo m’nkhalango usiku. Nyalugwe wagona mu mtengo pamwamba pake.

YESANI IZI: Ŵelengani Ezekieli 34:​25, ndipo yelekezani kuti muli ku malo a mtendele ofotokozedwa pa lembali.—kr 236 ¶16.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 14:1—Kodi maganizo ochulidwa pa lembali angakhudze bwanji ngakhale Akhristu? (w13 9/15 19 ¶12)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 13:1–14:7 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Muitanileni ku Cikumbutso. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 1) NYUMBA NA NYUMBA. Muitanileni ku Cikumbutso. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)

6. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) NYUMBA NA NYUMBA. Munthu waonetsa cidwi atapatsidwa kapepala koitanila ku Cikumbutso. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)

7. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 13 cidule cake, mafunso obweleza, komanso colinga. Seŵenzetsani nkhani yopezeka pa mbali yakuti “Fufuzani” kuti muthandize wophunzila kumvetsa mmene Mulungu amaonela zipembedzo zonyenga. (th phunzilo 12)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 8

8. “Nzelu Ziposa Zida Zomenyela Nkhondo”

(Mph. 10) Kukambilana.

Tate wa m’vidiyo yakuti “Tengelani Citsanzo ca Anthu Acikhulupililo, Osati Opanda Cikhulupililo​—Inoki, Osati Lameki,” akusinkhasinkha zimene aŵelenga m’Baibo. M’maganizo mwake akuona Inoki atabisala m’phanga pomwe amuna amikondo akumufuna-funa.

Zaciwawa zikuwonjezeka padziko lonse. Yehova adziŵa kuti kuculuka kwa ciwawa kungatibweletsele nkhawa yaikulu. Ndipo amamvetsa kuti timafunikila citetezo. Imodzi mwa njila zimene Mulungu amatitetezela ni Mawu ake, Baibo.—Sal. 12:​5-7.

M’Baibo muli nzelu zopambana “zida zomenyela nkhondo.” (Mla. 9:18) Onani mmene mfundo zotsatilazi za m’Baibo zingatithandizile kupewa zaciwawa.

  • Mla. 4:​9, 10—Pewani kukhala muli nokha-nokha ku malo osatetezeka

  • Miy. 22:3—Mukakhala pakati pa anthu muzionetsetsa zimene zikucitika

  • Miy. 26:17—Pewani kuloŵelela mikangano yosakukhudzani

  • Miy. 17:14—Cokani pa malopo mukaona kuti pangacitike zaciwawa. Pewani kukhala pa gulu la anthu amene afuna kucita zionetselo zosakondwa

  • Luka 12:15—Musayike moyo wanu paciwopsezo pofuna kuteteza zinthu zanu

Tambitsani VIDIYO yakuti Tengelani Citsanzo ca Anthu Acikhulupililo, Osati Opanda Cikhulupililo—Inoki, Osati Lameki. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi citsanzo ca Inoki cinakhudza bwanji zisankho komanso zocita za tate wa mu vidiyo pa nthawi ya ciwawa?—Aheb. 11:5

Pa zocitika zina, Mkhristu angafunikile kucita zonse zotheka kuti adziteteze kapena kuteteza katundu wake. Zikatelo, iye angafunike kuyesetsa kupewa kupha munthu kuti asakhale na mlandu wa magazi.—Sal. 51:14; onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Mlonda ya July 2017.

9. Kuitanila Anthu ku Cikumbutso Kudzayamba pa Ciŵelu, March 2

(Mph. 5) Ikambidwe na mkulu. Fotokozani makonzedwe a pampingo panu okhudza kampeni, nkhani yapadela, na Cikumbutso. Kumbutsani ofalitsa kuti angasankhe kucitako upainiya wa maola 15 m’miyezi ya March na April.

10. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu. 6 ¶9-17

Mawu Othela (Mph. 3)| Nyimbo 40 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani