LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 September masa. 6-7
  • September 23-29

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • September 23-29
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 September masa. 6-7

SEPTEMBER 23-29

MASALIMO 88-89

Nyimbo 22 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Ulamulilo wa Yehova Ni Wabwino Koposa

(Mph. 10)

Ulamulilo wa Yehova udzabweletsa cilungamo ceni-ceni (Sal. 89:14; w17.06 28 ¶5)

Ulamulilo wa Yehova udzathandiza anthu kukhala na cimwemwe ceniceni (Sal. 89:15, 16; w17.06 29 ¶10-11)

Ulamulilo wa Yehova udzakhalapo kwamuyaya (Sal. 89:34-37; w14 10/15 10 ¶14)

Zithunzi: M’bale akuganizila ulamulilo wa Yehova poyelekezela na ulamulilo wa anthu. 1. Anthu akukangana pa msonkhano wa zandale. 2. Abale akupatsana moni mwacimwemwe pa msonkhano wa mpingo.

Kuganizila kwambili ulamulilo wabwino koposa wa Yehova kungatithandize kusakhalila mbali pa zandale tikamva mfundo zokopa za andale

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 89:37​—Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kudalilika na kukhulupilika? (cl-CN 281 ¶4-5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 89:1-24 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Pemphani munthu amene si wacipembedzo ca Cikhristu kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 5 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. M’pempheni kuti mumuonetse mmene phunzilo la Baibo limacitikila. (th phunzilo 9)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Nkhani. ijwbq-CN 181​—Mutu: Kodi Baibo Imakamba Zotani? (th phunzilo 2)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 94

7. Mfundo za Yehova Ni Zabwino Koposa

(Mph. 10) Kukambilana.

Anthu ambili amaona kuti Baibo imakhwimitsa zinthu pa nkhani ya kugonana komanso ukwati, ndiponso kuti mfundo zake n’zacikale-kale. Kodi ndinu wotsimikiza kuti kutsatila mfundo ya Yehova kumacititsa kuti zinthu zikuyendeleni bwino nthawi zonse?​—Yes. 48:17, 18; Aroma 12:2.

    Zithunzi za m’vidiyo yakuti “Zifukwa Zokhalila na Cikhulupililo​​—Niziyendela mfundo za Mulungu Kapena Zanga?” Hugo na Clara.
  • N’cifukwa ciyani sitiyenela kudalila mfundo za dzikoli za makhalidwe abwino? (Yer. 10:23; 17:9; 2 Akor. 11:13-15; Aef. 4:18, 19)

  • Zithunzi: Zithunzi zojambula za m’vidiyo yakuti “Zifukwa Zokhalila na Cikhulupililo​​—Niziyendela mfundo za Mulungu Kapena Zanga?” 1. Tabuleti ikuonetsa cidindo ca jw.org. 2. Hugo akuŵelenga Baibo pa foni yake ali m’basi. 3. Clara akupemphela.
  • N’cifukwa ciyani tiyenela kudalila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino? (Yoh. 3:16; Aroma 11:33; Tito 1:2)

Baibo imaphunzitsa kuti onse amene samvela malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino “sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.” (1 Akor. 6:9, 10) Koma kodi ici ndiye cifukwa cokha cotsatilila mfundo za Mulungu?

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Zifukwa Zokhalila na Cikhulupililo—Niziyendela Mfundo za Mulungu Kapena Zanga? Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino zimatiteteza bwanji?

8. Zofunikila za Mpingo

(Mph. 5)

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 15 ¶15-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 133 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani