LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 September masa. 14-15
  • October 28–November 3

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • October 28–November 3
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 September masa. 14-15

OCTOBER 28–NOVEMBER 3

MASALIMO 103-104

Nyimbo 30 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Iye Amakumbukila “Kuti Ndife Fumbi”

(Mph. 10)

Khalidwe la cifundo limapangitsa Yehova kukhala wololela (Sal. 103:8; w23.07 21 ¶5)

Iye samatisiya tikalakwitsa (Sal. 103:9, 10; w23.09 6-7 ¶16-18)

Iye satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse (Sal. 103:14; w23.05 26 ¶2)

Mwamuna akumvetsela mwa chelu pamene mkazi wake akufotokoza nkhawa zake.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimakhala wololela pocita zinthu na mnzanga wa mu ukwati potengela citsanzo ca Yehova?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 104:24​—Kodi vesiyi itiphunzitsa ciyani za mphamvu za kulenga za Yehova? (cl-CN 55 ¶18)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 104:1-24 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Kambilanani vidiyo yakuti Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo na munthu amene anavomela kuphunzila Baibo. (th phunzilo 9)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 6​—Mutu: Mwamuna ayenela kukonda mkazi wake “mmene amadzikondela yekha.” (th phunzilo 1)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 44

7. Kodi Mumadziŵa Zimene Simungakwanitse Kucita?

(Mph. 15) Kukambilana.

Yehova amakondwela tikamacita zonse zimene tingathe pomutumikila ndipo nafenso timasangalala. (Sal. 73:28) Komabe, pamene tikuyesetsa kucita zimene tingathe, tiyenelanso kukumbukila kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse. Tikatelo, tidzapewa kukhala na nkhawa komanso kukhumudwa.

Mlongo wacitsikana wa m’vidiyo yakuti “Tingacite Zambili mwa Kuyembekezela Zinthu Zotheka.”

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Tingacite Zambili mwa Kuyembekezela Zinthu Zotheka. Ndiyeno funsani omvela kuti:

  • Kodi Yehova amafuna kuti tizicita ciyani? (Mika 6:8)

  • Cinthunzi ca m’vidiyo yakuti “Tingacite Zambili mwa Kuyembekezela Zinthu Zotheka.” Mlongo wacitsikana uja pamodzi na mnzake akulimbikitsa wophunzila Baibo pa lesitilanti.
  • N’ciyani cinathandiza mlongo wacitsikana kuti acepetseko nkhawa imene anali nayo yofuna kukwanilitsa colinga cake?

KODI TINGADZIŴE BWANJI ZIMENE TINGAKWANITSE KUCITA?

  • Pewani kudziyelekezela na ena. (Agal. 6:4) Musaone kuti mungakwanitse kucita zina zake cifukwa anthu ena amakwanitsa kucita zinthuzo. Nthawi zina, mungacite zambili kuposa munthu amene mufanana naye msinkhu kapena wocokela m’banja lofanana na lanu. Koma nthawi zinanso, iye ndiye angacite zoposa

  • Musalole kuti mantha akulepheletseni kucita zinthu zatsopano. (Aroma 12:1; 1 Akor. 7:31) Musacite mantha kuyamba utumiki umene poyamba ungaoneke wovuta kapena wosasangalatsa​—Mal. 3:10

  • Dziŵani zimene mungakwanitse kucita mwa kudziikila zolinga zing’ono-zing’ono. Mwacitsanzo, kodi mungakwanitse kucitako upainiya wokhazikika? Mwina kwa miyezi ingapo, mungawonjezele nthawi imene mumathela mu ulaliki kapena kucitako upainiya wothandiza. Kodi mungaciteko upainiya wokhazikika kwa caka cimodzi? Ngakhale mutaona kuti simungakwanitse kukhala mpainiya wokhazikika kapena kuyesako kwa caka cimodzi, mudzakondwela kwambili cifukwa cokwanilitsa zolinga zing’ono-zing’ono zimene munadziikila.​—Mla. 6:9

  • Khalani wokonzeka kusintha. Zinthu pa umoyo zimasintha, nazonso zimene timakwanitsa kucita zimasintha. Conco, nthawi na nthawi unikaninso zolinga zanu

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu. 17 ¶8-12, bokosi pa tsa. 137

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 55 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani