LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 January masa. 10-11
  • February 10-16

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • February 10-16
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 January masa. 10-11

FEBRUARY 10-16

MASALIMO 147-150

Nyimbo 12 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Wamasalimo akuyang’ana nyenyezi kumwamba uku akutamanda Yehova. Ndipo kacisi wa ku Yerusalemu ali capafupi.

1. Tili na Zifukwa Zambili Zotamandila Ya

(Mph. 10)

Amatisamalila aliyense payekha-payekha (Sal. 147:​3, 4; w17.07 18 ¶5-6)

Amamvetsa mmene timamvela ndipo amaseŵenzetsa mphamvu zake potithandiza (Sal. 147:5; w17.07 18 ¶7)

Watipatsa mwayi wapadela wokhala pakati pa anthu ake (Sal. 147:​19, 20; w17.07 21 ¶18)


DZIFUNSENI KUTI, ‘N’ciyaninso cina cimene cimanilimbikitsa kutamanda Yehova?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 148:​1, 10​—Kodi “mbalame zamapiko” zimatamanda Yehova m’njila yotani? (it-1-E 316)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 148:1–149:9 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KU NYUMBA NA NYUMBA. Munthu wakuuzani kuti ali na matenda aakulu. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pezani njila youzilako munthu zimene munaphunzila pa msonkhano waposacedwa. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) w19.03 10 ¶7-11​—Mutu: Mvelani Yesu mwa Kulalikila Uthenga Wabwino. Onani cithunzi. (th phunzilo 14)

Mwamuna na mkazi akulalikila mwamuna amene ali pa gombe.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 159

7. Lipoti la Caka ca Utumiki

(Mph. 15) Kukambilana.

Pambuyo poŵelenga cilengezo cocokela ku ofesi ya nthambi cokhudza lipoti la caka ca utumiki, pemphani omvela kuti achuleko zina mwa zinthu zocititsa cidwi za mu Lipoti la Caka ca Utumiki ca 2024 la Mboni za Yehova pa Dziko Lonse. Funsani mafunso ofalitsa amene munawakonzekeletsa pasadakhale kuti asimbe zocitika zolimbikitsa za mu ulaliki za m’caka ca utumiki capita.

Abale na alongo akulalikila m’malo osiyanasiyana padziko lapansi. Akulalikila uthenga wabwino pogwilitsa nchito tumasitandi twa ulaliki, kupitila pa vidiyo konfalensi, kunyumba na nyumba, komanso poseŵenzetsa njila zina.

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 22 ¶7-14, mabokosi pa masa. 174, 177

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 37 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani