Yophunzila
AUGUST 2021
NKHANI ZOPHUNZILA: SEPTEMBER 27–OCTOBER 31, 2021
© 2021 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika pa dziko lonse lapansi. Nchito imeneyi timaiyendetsa na zopeleka zaufulu. Kuti mupange copeleka, pitani pa donate.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.
CITHUNZI CA PACIKUTO:
Banja likulalikila kudela limene kuli alengezi a Ufumu ocepa; mlongo wacitsikana akuthandizila pa nchito yomanga Nyumba ya Ufumu; banja lokalamba likucita ulaliki wa pafoni. Onse akupeza cimwemwe mu utumiki wawo (Onani nkhani yophunzila 34, ndime 11)