LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 January tsa. 32
  • Jambulani Kuti Mukumbukile

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Jambulani Kuti Mukumbukile
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Nkhani Zofanana
  • “Kuyandikila kwa Mulungu Ndi Cinthu Cabwino” kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Kuseŵenzetsa Bwino Zitsanzo Zooneka
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 January tsa. 32

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU

Jambulani Kuti Mukumbukile

Monga mmene zilili kwa anthu ambili, n’kutheka kuti nanunso zimakuvutani kukumbukila zimene mwangowelenga kumene. Komabe, n’kosavuta kukumbukila zinthu zambili zimene Yesu anaphunzitsa, cifukwa nthawi zambili anali kugwilitsa nchito mafanizo. Mungakwanitse kuziona m’maganizo mwanu zimene iye anaphunzitsa, ndipo izi zimakuthandizani kuti musamaiwale zinthuzo. Mofananamo, mungamakumbukile zambili zimene mumawelenga mwa kupanga zithunzi m’maganizo mwanu. Kodi mungacite bwanji zimenezi? Mungatelo mwa kujambula zithunzi pamene mukuwelenga.

Anthu amene amajambula zithunzi za zinthu zatsopano zimene aphunzila, amakumbukila zinthuzo mosavuta. Amaona kuti kuphunzila mwa njila imeneyi kumawathandiza kumvetsa osati cabe mawu, koma kumawathandizanso kumvetsa mfundo zikuluzikulu zimene aphunzila. Zithunzi zimenezi sizikhala zaukatswili, koma zimakhala zosavuta komanso zosacolowana. Umboni uonetsa kuti kujambula zithunzi kumakhala kothandiza makamaka kwa acikulile kukumbukila zimene acoka kuwelenga.

Pa kuwelenga kwanu kotsatila, mungayese kujambula zithunzi za zinthu zimene mwawelenga. Mungadabwe ndi kuculuka kwa zinthu zimene mudzatha kukumbukila!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani