LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 July tsa. 31
  • Kodi Mudziwa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudziwa?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Nkhani Zofanana
  • Yamikilani Mwayi Wanu Wolambila Yehova M’kacisi Wake Wauzimu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 July tsa. 31
Ansembe akupeleka nsembe za nyama pa guwa lansembe la pa kacisi.

Kodi Mudziwa?

M’zaka za zana loyamba, ndi motani mmene ansembe a pa kacisi anali kutayila magazi a nyama zimene zapelekedwa nsembe?

CAKA ciliconse, ansembe mu Isiraeli wakale anali kupeleka nsembe za nyama masauzande pa guwa lansembe la pa kacisi. Josephus, wolemba mbili waciyuda wa m’zaka za zana loyamba anakamba kuti pa Pasika, nkhosa zoposa 250,000 zinali kupelekedwa nsembe. Izi zinali kucititsa kuti pa guwa lansembe pazikhala magazi ambili. (Lev. 1:​10, 11; Num. 28:​16, 19) Kodi magazi amenewo anali kupita kuti?

Akatswili ofukula zinthu zakale apeza ngalande yaikulu m’kacisi wa Herode imene inali kugwilitsidwa nchito mpaka pamene kacisiyo anawonongedwa mu 70 C.E. Mwacionekele, ngalande imeneyi ndi mmene munali kudutsa magazi a nyama zimene zapelekewa nsembe.

Tiyeni tikambilane zinthu ziwili zimene zinali kuthandizila kuti guwa lansembe likhale loyela:

  • Mibowo imene unali pansi pa guwa lansembe: Buku la Mishnah lifotokoza mmene ngalande za pa guwa lansembe zinali kugwilila nchito. Bukuli lili ndi miyambo yaciyuda komanso malamulo apakamwa, ndipo linalembedwa pambuyo pa caka ca 200 C.E. Bukuli limafotokoza kuti panali mibowo iwili pakona limodzi la guwa lansembe. Ndipo magazi a nyama zopelekedwa nsembe komanso madzi amene anali kugwilitsidwa nchito poyeletsa guwalo, anali kudutsa m’mibowo imeneyo kupita m’ngalande yopita ku Cigwa ca Kidironi.

    Ofukula zinthu zakale amagwilizana ndi zimene zinafotokozedwa m’buku lakale limeneli. Buku lakuti The Cambridge History of Judaism limacitila umboni pa zimene zinapezeka zokhudzana ndi ngalande zomwe zinapezeka pafupi ndi pomwe panali kacisi. Bukuli limati: “Mwacionekele, m’ngalandezi ndi mmene munali kudutsa madzi osakanikilana ndi magazi a nyama zimene zapelekedwa nsembe pa kacisi.”

  • Pa kacisi panali kukhala madzi okwanila: Ansembe anali kufunikila madzi ambili kuti aziyeletsela guwa lansembe komanso ena othandizila kuti magazi azidutsa m’ngalande mosavuta. Kuti acite nchito yofunika imeneyi, nthawi zonse iwo anali kukhala ndi madzi ocokela mumzinda amene anali kugwilitsa nchito. Madziwo anali kupita ku kacisi kudzela m’ngalande, ndipo anali kuwasungila m’zitsime komanso m’maiŵe. Katswili wina wofukula za m’mabwinja, Joseph Patrich, anati: “Zikuoneka kuti pa nthawiyo, ndi kacisi yekhayu amene anali ndi dongosolo labwino conci lopezela madzi komanso locotsela madzi adothi.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani