MAU A M’BAIBO
Yesu “Anaphunzira Kumvera”
Yesu nthawi zonse wakhala akumvera Yehova. (Yoh. 8:29) Ndiye n’cifukwa ciani Baibo imakamba kuti: “[Iye] anaphunzira kumvera cifukwa ca mabvuto amene anakumana nao”?—Aheb. 5:8.
Yesu ali padziko lapansi, anakhala umoyo wosiyana ndi umene anali nao kumwamba. Analeredwa ndi makolo opanda ungwiro amene anali odzipereka kwa Mulungu. (Luka 2:51) Iye anapirira pamene anali kuzunzidwa ndi atsogoleri acinyengo a cipembedzo ndi akulu-akulu a boma opanda cilungamo. (Mat. 26:59; Maliko 15:15) Kuonjezera apo, iye “anadzicepetsa ndipo anakhala womvera mpaka imfa,” inde, imfa yowawa.—Afil. 2:8.
Zimene Yesu anakumana nazozi zinam’phunzitsa kukhala womvera m’njira imene sanaphunzirepo ali kumwamba. Izi zinam’cititsa kuti akhale Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wabwino koposa, wokhoza kumvetsa mabvuto athu. (Aheb. 4:15; 5:9) Yesu anakhala wamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova ataphunzira kumvera cifukwa ca mabvuto amene anakumana nao. Nafenso tingakhale a mtengo wapatali kwambiri kwa Yehova komanso ofunika kwa iye tikakhalabe omvera tikakumana ndi mabvuto.—Yak. 1:4.