Zamkati
February 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MLUNGU WA APRIL 4-10, 2016
3 Yehova Anamucha kuti “Bwenzi Langa”
MLUNGU WA APRIL 11-17, 2016
9 Tengelani Citsanzo ca Mabwenzi Apamtima a Yehova
Nkhanizi zidzatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. M’nkhani yoyamba, tidzakambilana citsanzo ca Abulahamu. M’nkhani yaciŵili, tidzakambilana citsanzo ca Rute, Hezekiya, ndi Mariya mai a Yesu.
MLUNGU WA APRIL 18-24, 2016
14 Khalani Wokhulupilika kwa Yehova
MLUNGU WA APRIL 25, 2016–MAY 1, 2016
20 Tengelani Citsanzo ca Atumiki Okhulupilika a Yehova
M’nkhani ziŵilizi, tidzakambilana zocitika za m’Baibulo zokhudza Mfumu Davide ndi ena amene analiko m’nthawi yake. Pamene tikambilana zitsanzo zao, tidzaona zimene zingatithandize kukhalabe okhulupilika kwa Yehova ngakhale panthawi zovuta.
CITHUNZI CA PACIKUTO:
BENIN
Ku mudzi wa Hetin, nyumba zambili anazimanga pamwamba pa mitengo kuti madzi asamaloŵe. Anthu amagwilitsila nchito mabwato aang’ono akafuna kuyenda ulendo waufupi. Ofalitsa 215 ndi apainiya 28 a m’mipingo itatu ya m’mudziwo, anasangalala kwambili pamene anthu 1,600 anapezeka pa Cikumbutso mu 2014
KULI ANTHU
10,703,000
OFALITSA
12,167
APAINIYA A NTHAWI ZONSE