Zamkati
MLUNGU WA JUNE 27, 2016–JULY 3, 2016
3 Tizithetsa Mikangano Mwamtendele
Popeza ndife opanda ungwilo, nthawi zina timasemphana maganizo ndi abale ndi alongo athu. M’nkhaniyi, tidzaphunzila mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuthetsa mikangano ndi kukhala pa mtendele ndi anthu ena.
MLUNGU WA JULY 4-10, 2016
9 “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse Kuti Akhale Ophunzila”
Nkhaniyi idzatithandiza kumvetsetsa cifukwa cake timakamba kuti Mboni za Yehova ndizo zokha padziko lapansi zimene zikukwanilitsa ulosi wa Yesu wa pa Mateyu 24:14. Tidzaphunzilanso zimene kukhala “asodzi a anthu” kumatanthauza.—Mateyu 4:19.
MLUNGU WA JULY 11-17, 2016
15 Kodi Mumasankha Bwanji Zocita?
Pamene mukupanga zosankha, kodi mumangosankha zimene muona kuti n’zoyenela? Kapena mumapempha ena kuti akuuzeni zocita? Nkhaniyi ifotokoza mmene tingapangile zosankha zabwino mwa kuganizila mmene Yehova Mulungu amaonela zinthu.
MLUNGU WA JULY 18-24, 2016
21 Kodi Baibulo Likusinthabe Umoyo Wanu?
N’kutheka kuti munapanga masinthidwe aakulu musanabatizidwe. Koma kodi muona kuti masiku ano zimakuvutani kusintha zinthu zing’onozing’ono kuti mutengele citsanzo ca Yehova ndi Yesu? Nkhaniyi ifotokoza cifukwa cake zingakhale zovuta kusintha ndiponso mmene Baibulo lingatithandizile.
MLUNGU WA JULY 25-31, 2016
27 Pindulani Mokwanila ndi Cakudya Cakuuzimu Cimene Yehova Amapeleka
M’nkhani ino, tikambilana maganizo amene tiyenela kupewa, ndiponso mmene tingapindulile ndi cakudya cakuuzimu cimene Yehova amatipatsa.