LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g19 na. 1 masa. 12-15
  • Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko “Padzakhala Mtendele Woculuka”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko “Padzakhala Mtendele Woculuka”
  • Galamuka!—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI UFUMU WA MULUNGU UDZABWELA LITI?
  • KODI UFUMU WA MULUNGU UDZALAMULILA MOTANI?
  • KODI MUNGAPINDULE BWANJI NA ULAMULILO WA UFUMU UMENEWU?
  • Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Ufumu Wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Ciyembekezo
    Galamuka!—2018
Onaninso Zina
Galamuka!—2019
g19 na. 1 masa. 12-15
Anthu akukondwela na moyo m’paradaiso

MMENE MTENDELE WENI-WENI UDZABWELELA PA DZIKO

Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko “Padzakhala Mtendele Woculuka”

Posacedwa, Ufumu wa Mulungu umene tauyembekezela kwa nthawi yaitali, kapena kuti boma la pa dziko lonse lokhadzikitsidwa na Mulungu, lidzabweletsa mtendele na mgwilizano pa dziko lonse lapansi. Malinga na lonjezo la pa Salimo 72:7, pa dziko “padzakhala mtendele woculuka.” Kodi Ufumu wa Mulungu udzayamba liti kulamulila pa dziko lapansi? Kodi Ufumu wa Mulungu udzalamulila motani? Nanga mungapindule bwanji na ulamulilo wake?

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZABWELA LITI?

Baibo inakambilatu zinthu zina zocititsa cidwi, zimene zidzakhala cizindikilo cakuti Ufumu wa Mulungu wayandikila. Nkhondo pakati pa maiko, njala, matenda, kuculuka kwa zivomezi, na kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, zonsezi ni “cizindikilo.”—Mateyu 24:3, 7, 12; Luka 21:11; Chivumbulutso 6:2-8.

Baibo inaloselanso kuti: “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale awo, osafuna kugwilizana ndi anzawo, onenela anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, . . . odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-4) Ndipo nthawi zonse makhalidwe amenewa akhala akuonekela mwa anthu ena. Koma masiku ano akuonekela mwa anthu ambili.

Maulosi amenewa anayamba kukwanilitsidwa mu 1914. Akatswili olemba mbili yakale, andale ochuka, komanso olemba mabuku, onse akambapo za mmene dziko linasinthila m’caka cimeneco. Mwacitsanzo, wolemba mbili yakale Peter Munch wa ku Denmark analemba kuti: “M’mbili yonse ya anthu, nkhondo ya mu 1914 inasintha zinthu kwambili. Cisanafike cakaci, zinthu zinali kusinthila kuubwino. Koma mwadzidzidzi, tinaloŵa m’nthawi ya mavuto aakulu, monga cidani, nkhawa, komanso kusoŵa kwa citetezo pa dziko lonse.”

Koma kumbali ina, zocitika zimenezi ni cizindikilo cakuti zinthu zabwino zili pafupi. Zimaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kuyamba kulamulila pa dziko lonse lapansi. Ndipo Yesu anakambanso mbali ina yabwino ya cizindikilo ca mapeto. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.

Uthenga wabwino umenewu, ndiye nkhani yaikulu ya uthenga umene Mboni za Yehova zimalalikila. Ndipo magazini yawo imene imafalitsidwa kwambili, inalembedwa kuti Nsanja ya Mlonda, Imalengeza za Ufumu wa Yehova. Lomba, imapezeka m’vitundu vopitilila 338. Kaŵili-kaŵili, Nsanja ya Mlonda imafotokoza zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzacitila anthu, komanso dziko lapansi.

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZALAMULILA MOTANI?

Yankho lake imapezeka na mbali zinayi izi zofunikila:

  1. Ufumu wa Mulungu sudzalamulila kupitila mwa atsogoleli andale a dzikoli.

  2. Cifukwa ca dyela lawo, atsogoleli andale sadzafuna kutula pansi ulamulilo. Iwo mopanda nzelu adzayesa kulimbana na Ufumu wa Mulungu.—Salimo 2:2-9.

  3. Ufumu wa Mulungu udzacita kuwononga maufumu amene akufuna kupitiliza kupondeleza anthu. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 19:17-21) Nkhondo yothela ya pa dziko lonse imeneyi imachedwa Aramagedo.—Chivumbulutso 16:14, 16.

  4. Anthu onse amene amagonjela ku ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu, adzapulumutsidwa pa nkhondo ya Aramagedo na kuloŵa m’dziko latsopano lamtendele. Baibo imawachula kuti “khamu lalikulu,” ndipo mwina ciŵelengelo cawo cidzafika m’mamiliyoni.—Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14.

    KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACITA CIANI?

    Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anaonetsa dyonkho cabe la zimene adzacita monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Anacilitsa odwala na olemala. (Mateyu 4:23) Anadyetsa anthu masauzande ambili. (Maliko 6:35-44) Ndipo iye analamulilanso cilengedwe. —Maliko 4:37-41.

    Yesu akuphunzitsa anthu

    Koposa zonse, Yesu anaphunzitsa anthu mmene angakhalile mwa mtendele komanso ogwilizana. Onse amene modzicepetsa amaseŵenzetsa zimene Yesu anaphunzitsa, amakhala na makhalidwe abwino amene adzaŵathandiza kukhala na umoyo wacimwemwe mu Ufumu wake. Palibe mphunzitsi wina aliyense angakwanilitse zimenezi. Zina mwa zimene Yesu anaphunzitsa mungazipeze mu Mateyu macaputa 5 mpaka 7. Ulaliki umenewu umadziŵika kuti Ulaliki wa pa Phili. Bwanji osaŵelenga macaputa amenewa? Mawu ake si ozama. Koma uthenga wake ni wothandiza kwambili. Ndipo umafikadi pamtima.

KODI MUNGAPINDULE BWANJI NA ULAMULILO WA UFUMU UMENEWU?

Kuti munthu akhale nzika ya Ufumu wa Mulungu, coyamba afunika kuphunzila. M’pemphelo lake kwa Mulungu, Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Anthu akam’dziŵa bwino Yehova Mulungu kuti ni weni-weni, amapindula m’njila zambili. Onani njila ziŵili izi: Yoyamba, iwo amakhala na cikhulupililo colimba mwa iye. Cikhulupililo cozikidwa pa umboni cimeneco, cimaŵatsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu ni weni-weni, ndipo ulamulilo wake uli pafupi. (Aheberi 11:1) Yaciŵili, iwo amakulitsa cikondi cawo pa Mulungu ndi anthu. Cikondi pa Mulungu cimaŵalimbikitsa kumumvela na mtima wonse. Cikondi pa anthu cimaŵalimbikitsa kuseŵenzetsa zimene Yesu anakamba kuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inuyo muwacitile zomwezo.”—Luka 6:31.

Mofanana na tate wacikondi, Mlengi wathu amatifunila zabwino. Amafuna kuti tikhale na umoyo umene Baibo imati, ‘umoyo weni-weni.’ (1 Timoteyo 6:19) Umoyo masiku ano si ‘umoyo weni-weni.’ Kwa anthu ambili umoyo ni wovuta kwambili, cakuti amavutika kuti apeze zofunikila za pa umoyo. Kuti mukhale na cithunzi ca mmene ‘umoyo weni-weni’ udzakhalila, onani zinthu zina zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzacitila nzika zake.

MMENE UMOYO WENI-WENI UDZAKHALILA

  • “M’masiku ake, [mu ulamulilo wa Khristu monga Mfumu] wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendele woculuka . . . Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjela . . . kukafika kumalekezelo a dziko lapansi.” —Salimo 72:7, 8, 13, 14.

  • “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo.”—Salimo 46:9.

  • “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.” —Salimo 72:16.

  • “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. . . . Anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.

  • “Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Anthu akukondwela na moyo m’paradaiso

Mu ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu, anthu adzakhala otetezeka komanso pa mtendele. Ndipo adzakhala na cakudya coculuka

MFUNDO YAIKULU

ZIMENE YESU ANAPHUNZITSA ZIMALIMBIKITSA ANTHU KUCITA ZOYENELA. MU BOMA LAKE LA PA DZIKO LONSE, ONSE AMENE AMATSATILA ZIMENE YESU ANAPHUNZITSA ADZAKHALA OGWILIZANA KWAMBILI, NDIPO ADZAKHALA PA MTENDELE

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani