LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g19 na. 2 masa. 4-5
  • Mapindu a Kudziletsa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mapindu a Kudziletsa
  • Galamuka!—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI KUDZILETSA KUMATANTHAUZA CIANI?
  • N’CIFUKWA CIANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?
  • HMMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KUDZILETSA
  • Phunzilani Kukhala Wodziletsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Kudziletsa—N’kofunika Kuti Tikondweletse Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Galamuka!—2019
g19 na. 2 masa. 4-5
Aletsa mwana wawo kutenga maswiti m’shopu

PHUNZILO 1

Mapindu A Kudziletsa

KODI KUDZILETSA KUMATANTHAUZA CIANI?

Kudziletsa kumatanthauza kukwanitsa

  • kuyembekezela moleza mtima zinthu zina

  • kuugwila mtima

  • kutsiliza nchito imene siikukondweletsani

  • kuika zofuna za ena patsogolo

N’CIFUKWA CIANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?

Ana amene ni odziletsa kwambili, amakwanitsa kukaniza mayeselo olo kuti angaoneke othandiza kwa kanthawi. Koma ana amene sakwanitsa kweni-kweni kudziletsa, kaŵili-kaŵili akakula amakhala

  • aciwawa

  • ovutika maganizo

  • okoka fodya kapena kumwa moŵa mwaucidakwa, kapenanso kuseŵenzetsa amkolabongo

  • osakonda kudya zakudya zamagulu onse

Kafuku-fuku wina anapeza kuti aja amene anali odziletsa pamene anali ana, sakhala na mavuto ambili okhudza thanzi komanso nkhawa ya zandalama. Ndipo savutika kutsatila malamulo a boma. Pambuyo pa kafuku-fuku umenewo, Pulofesa wina dzina lake Angela Duckworth wa pa Yunivesiti ya Pennsylvania anati: “Sipangakhale pomveka kukamba kuti kukhala wodziletsa n’koipa.”

HMMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KUDZILETSA

Mukati ayi, azikhaladi ayi.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Mateyu 5:37.

Nthawi zina mwana angayambe kulila kapena kuvuta ngakhale pakati pa anthu, n’colinga cofuna kuti makolo ake asinthe maganizo pa zimene akamba. Ngati kholo ligonja mwana wawo akacita zimenezi, ndiye kuti amuphunzitsa kuti kuvuta kapena kulila ni njila yabwino yakuti kholo lake lisinthe maganizo, kuti ayi wawo akhale inde.

Koma ngati kholo limatsimikizila kuti likakamba kuti ayi ni ayi, mwana amaphunzila mfundo yofunika mu umoyo yakuti, sitingakhale na zonse zimene tifuna. Dr. David Walsh analemba kuti: “Anthu odziletsa ndiye amakhala na umoyo wokhutila kwambili. Si cikondi kuphunzitsa ana athu kuti angakhale na zilizonse zimene afuna.”a

Kusapatsa mwana wanu ciliconse cimene wafuna, kudzam’thandiza kukhala wodziletsa akadzakula. Mwacitsanzo, adzakana kuseŵenzetsa am’kolabongo, kugonana asanaloŵe m’cikwati, kapena kuloŵa m’makhalidwe ena oipa.

Thandizani ana anu kumvetsa zotulukapo zabwino, kapena zoipa pa zimene angacite.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.”—Agalatiya 6:7.

Mwana wanu afunika kudziŵa kuti zilizonse zimene angacite zili na zotulukapo zake. Ndipo kusadziletsa kungakhale na zotulukapo zoipa. Mwacitsanzo, ngati mwana wanu amakalipa msanga, ena angayambe kum’pewa. Koma ngati amadziletsa mwa kuugwila mtima akakhumudwitsidwa, kapena ngati amayembekeza moleza mtima ngati wina akamba, m’malo mom’dula mawu, anthu amam’konda. Conco, m’thandizeni kumvetsa kuti ngati amadziletsa, akakula adzakhala na umoyo wabwino.

Phunzitsani mwana wanu kuika patsogolo zinthu zofunika.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

Kudziletsa kumatithandiza kupewa kucita zinthu zoipa. Kumatithandizanso kucita zinthu zimene sitikonda kweni-kweni, koma zimene n’zofunika kuzicita. M’pofunika kuphunzitsa mwana wanu kuona kuti ni zinthu ziti zofunika kwambili, na kuti azicita zimenezo coyamba. Mwacitsanzo, angafunike kucita homuweki coyamba akalibe kuyamba kuseŵela.

Khalani citsanzo cabwino.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ndakupatsani citsanzo kuti mmene ine ndacitila kwa inu, inunso muzicita cimodzimodzi.” —Yohane 13:15.

Mwana wanu amaona zimene mumacita pakacitika zinthu zokukalipitsani. Onetsani mwa citsanzo canu kuti kudziletsa kumakhala na zotulukapo zabwino. Mwacitsanzo, ngati mwana wanu wacita zinthu zina zoipa, kodi mumacita zinthu mwaukali kapena mumakhala wodekha?

a Kucokela m’buku lakuti, No: Why Kids—of All Ages—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.

Aletsa mwana wawo kutenga maswiti m’shopu

APHUNZITSENI AKALI AANG’ONO

Kusapatsa mwana wanu ciliconse cimene wafuna, kudzam’thandiza kukhala wodziletsa akadzakula. Mwacitsanzo, adzakana kuseŵenzetsa am’kolabongo, kapena kuloŵa m’makhalidwe ena oipa

Aphunzitseni mwa Citsanzo Canu

  • Kodi mwana wanga amaniona kuti sinitaya mtima mwaukali pakacitika zinthu zokhumudwitsa?

  • Kodi nimamuuza mwana wanga cifukwa cake nimayesetsa kuthetsa mavuto modekha mtima?

  • Kodi mwana wanga anganifotokoze bwanji, monga waphuma ndi wamtima wapacala, kapena wodekha ndi wodziletsa?

Zimene Makolo Ena Anacita . . .

“Ngakhale kuti mwana wathu wamkazi tinali kumulola kukhumudwa na kukalipa, sitinamulole kuti azisoŵetsa ena mtendele cifukwa ca kukhumudwa kwake. Conco, ngati walephela kulamulila mkwiyo wake, tinali kum’cotsa pakati pa anthu kuti abwelenso mtima ukakhala pansi.”—Theresa.

“Ine na mkazi wanga, tinapangana kuti nthawi zonse ŵana ŵathu akacita zinthu zotikondweletsa, monga kudziletsa na kupilila pa zinthu zokhumudwitsa, tisamalephele kuwayamikila.”—Wayne.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani