LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 masa. 10-11
  • N’cifukwa Ciani Timavutika, Kukalamba, na Kufa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Timavutika, Kukalamba, na Kufa?
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Timavutika Cifukwa ca Zimene Makolo Athu Oyambilila Anacita
  • Timavutikanso Cifukwa ca Mizimu Yoipa
  • Nthawi Zina Timadzibweletsela Tokha Mavuto
  • Tili mu “Masiku Otsiliza”
  • Kodi Zoipa Komanso Mavuto Zinakhalako Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • N’cifukwa Ciani Pa Dziko Pali Mavuto Ambili Conco?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 1 masa. 10-11
Anthu osauka akuvutika cifukwa cosoŵa zinthu zofunikila pa umoyo.

N’cifukwa Ciani Timavutika, Kukalamba, na Kufa?

Mlengi wathu amationa kuti ndife ana ake. Conco safuna kuti tizivutika. Koma padzikoli pali mavuto ambili. N’cifukwa ciani zili conco?

Timavutika Cifukwa ca Zimene Makolo Athu Oyambilila Anacita

“Ucimo [unalowa] m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa uchimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse.”—AROMA 5:12.

Mulungu analenga makolo athu oyambilila Adamu na Hava na matupi angwilo komanso maganizo angwilo. Anawaika m’paradaiso pano padziko lapansi—malo okongola ochedwa munda wa Edeni. Iye anawauza kuti angadye zipatso zonse za m’mitengo ya m’mundamo, kupatulapo zipatso za mumtengo umodzi. Koma Adamu na Hava anasankha kudya zipatso za mumtengo woletsedwawo, ndipo limenelo linali chimo. (Genesis 2:15-17; 3:1-19) Cifukwa ca kusamvela kwawo, Mulungu anawatulutsa m’mundawo, ndipo anayamba kukumana na mavuto. M’kupita kwa nthawi, anabeleka ana, ndipo anawo anayambanso kuvutika. Onse anakalamba ndiponso anamwalila. (Genesis 3:23; 5:5) Timadwala, kukalamba, na kufa cifukwa ndife mbadwa za Adamu na Hava, makolo athu oyambilila.

Timavutikanso Cifukwa ca Mizimu Yoipa

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” —1 YOHANE 5:19.

“Woipayo” amene wachulidwa palembali amachedwa Satana. Iye ni colengedwa camzimu cosaoneka cimene cinapandukila Mulungu. (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) M’kupita kwa nthawi, zolengedwa zina zamzimu zinagwilizana na Satana. Zolengedwa zimenezo zimachedwa ziwanda. Mizimu yoipa imeneyi imaseŵenzetsa mphamvu zawo ponyengelela anthu kuti apandukile Mlengi wawo. Imasonkhezela anthu ambili kucita zinthu zoipa. (Salimo 106:35-38; 1 Timoteyo 4:1) Satana na ziwanda amakondwela kuvutitsa anthu.

Nthawi Zina Timadzibweletsela Tokha Mavuto

“Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.”—AGALATIYA 6:7.

Tonsefe timavutika cifukwa ca ucimo wobadwa nawo komanso ulamulilo wa Satana. Koma nthawi zina, anthu amadzibweletsela okha mavuto. Motani? Akacita zinthu zoipa kapena kupanga zisankho zolakwika, nthawi zambili amakolola mavuto. Koma ngati anthu amacita zinthu zabwino amakololanso zabwino. Mwacitsanzo, mwamuna komanso tate woona mtima, amene amagwila nchito molimbika na kukonda banja lake, amakolola zinthu zambili zabwino. Ndipo amakondweletsa banja lake. Koma munthu waulesi amene amachova njuga na kumwa moŵa mwaucidakwa, angasauke na kusaukitsa banja lake. Conco ni cinthu canzelu kumvela Mlengi wathu. Iye amafuna kuti tizikolola zinthu zambili zabwino, kuphatikizapo “mtendele woculuka.” —Salimo 119:165.

Tili mu “Masiku Otsiliza”

“[M’masiku] otsiliza . . . , anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvela makolo, . . . osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino.”—2 TIMOTEYO 3:1-5.

Masiku ano, anthu ambili ali na makhalidwe amene anakambidwilatu palembali. Makhalidwe awo ni umboni winanso wakuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza’ a dzikoli. Malemba anakambilatunso kuti m’masiku otsiliza ano kudzakhala nkhondo, njala, zivomezi zoopsa, na matenda. (Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11) Zinthu zimenezi zimabweletsa mavuto oculuka, ndipo zapha anthu ambili.

Tsopano Nili na Mtendele wa Maganizo

“Nili na zaka 19 n’napuwala, ndipo n’nauzidwa kuti izi zinacitika cifukwa ca zoipa zimene n’nacita nikalibe kubadwa. Zimenezi zinali kunivutitsa maganizo kwambili. Anthu ena ananiuza kuti Mulungu ndiye amacititsa kuti anthufe tizivutika. N’naona kuti zinali zosatheka kum’konda Mulungu wankhanza conco. N’taphunzila Baibo n’nadziŵa kuti Mlengi amatikonda, na kuti mngelo woipa wochedwa Satana ndiye amapangitsa mavuto ambili pa anthu. N’naphunzilanso kuti posacedwa, Mulungu adzawononga Satana na kukonza zonse zimene iye wawononga. Lomba nimam’konda kwambili Mulungu wabwino ameneyu, ndipo nili na mtendele wa maganizo.”—Sanjay.

Sanjay.

Phunzilani zambili:

Kuti mudziŵe zambili pa nkhani ya mavuto na zimene mungacite kuti muwapilile, pitani pa jw.org ku Chichewa na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO > KUVUTIKA.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani