LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g22 na. 1 masa. 7-9
  • 2 | Tetezani Cuma Canu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 2 | Tetezani Cuma Canu
  • Galamuka!—2022
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA
  • Zimene Muyenela Kudziŵa
  • Zimene Mungacite Pali Pano
  • Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Moseŵenzetsela Ndalama
    Galamuka!—2019
Galamuka!—2022
g22 na. 1 masa. 7-9
Kalipentala akukhoma msomali.

DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU

2 | Tetezani Cuma Canu

CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Tsiku lililonse, anthu ambili amavutika kupeza zinthu zofunikila pa umoyo. N’zacisoni kuti mavuto aakulu a m’dzikoli, amapangitsa zimenezi kukhala zovuta kwambili. Cifukwa ciyani?

  • M’madela amene kwacitika matsoka aakulu, zinthu monga cakudya komanso pokhala zimakwela mtengo kwambili.

  • Izi zimapangitsa kuti anthu ambili azilandila malipilo ocepa kapenanso kucotsedwa nchito kumene.

  • Matsoka angawononge kapena kusokoneza mabizinesi a anthu, nyumba zawo, na katundu wawo. Ndipo izi zingapangitse ambili kukhala paumphawi.

Zimene Muyenela Kudziŵa

  • Ngati mumaseŵenzetsa bwino ndalama zanu, mudzakwanitsa kupilila pa nthawi ya mavuto.

  • Kumbukilani kuti citetezo ca ndalama sicokhalitsa. Ndalama zimene mumapeza, zimene mumasunga ku banki, na zinthu zanu zamtengo wapatali zingathe mphamvu.

  • Pali zinthu zina zimene ndalama siingagule, monga cimwemwe komanso mgwilizano wabanja.

Zimene Mungacite Pali Pano

Baibo imati: “Conco, pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.

Kukhala okhutila kumatanthauza kusalakalaka zambili, komanso kukhala wacimwemwe malinga ngati tili na zofunikila za tsiku na tsiku. Izi n’zofunika kwambili makamaka ngati tili na ndalama zocepa.

Kuti mukhale wokhutila, mungafunike kusinthako zinthu zina pa umoyo wanu. Ngati mumagula zinthu zodula kuposa ndalama zimene mumapeza, mudzakhala na mavuto aakulu a ndalama.

Pa nthawi ya mavuto aakulu, tetezani cuma canu mwa kucita izi

ZIMENE MUNGACITE Mfundo Zothandiza

CEPETSANI ZOGULA-GULA

  • Mzimayi wacikulile akuzula makaloti m’dimba lake.

    Cepetsani zogula-gula

    Musamangogula zilizonse koma zokhazo zomwe n’zofunikiladi. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nifunikadi kugula motoka? Kodi ningabzale ndiwo zamasamba m’malo mocita kukagula?’

  • Musanagule cinthu cina ciliconse, dzifunseni kuti: ‘Kodi n’cofunikiladi? Kodi ningakwanitse kucigula?’

  • Ngati n’zotheka pemphani thandizo ku boma kapena ku mabungwe ena othandiza anthu.

“Monga banja, tinakhala pansi na kuona mmene zinthu zinalili pa umoyo wathu. Tinacepetsako ndalama zimene tinali kugwilitsa nchito pocita zosangalatsa. Tinayambanso kukonza cakudya cosalila ndalama zambili.”—Gift.

PANGANI BAJETI

Mzimayi akuseŵenzetsa cipangizo coŵengetsela masamu polemba ndalama pa lisiti.

Pangani bajeti

Baibo imati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Bajeti idzakuthandizani kuti zimene mumagula zisamapitilile ndalama zimene mumapeza.

  • Coyamba, lembani ndalama zimene mumapeza pa mwezi.

  • Caciŵili, lembani zinthu zonse zimene mumagula pa mwezi, na kusanthula mosalama mmene mumaseŵenzetsela ndalama.

  • Kenako, yelekezelani zimene mumagula na ndalama zimene mumapeza. Ngati m’pofunikila, onani zimene mungacepetse kapena kucotselatu kuti ndalama zimene mumagwilitsa nchito zisamapitilile ndalama zimene mumapeza.

“Mwezi uliwonse, ine na mkazi wanga timalemba ndalama zimene tili nazo komanso zinthu zimene tifuna kugula. Timayesetsa kusungako ndalama ya zakugwa mwadzidzidzi komanso imene tingaseŵenzetse m’tsogolo. Kucita zimenezi, kumatithandiza kuti tisakhale na nkhawa kwambili cifukwa timadziŵa mmene tidzaseŵenzetsela ndalama zathu.”—Carlos.

PEWANI NKHONGOLE / MUZISUNGAKO NDALAMA

  • Mayi akuthandiza mwana wake wam’ngono kuika ndalama m’botolo.

    Pewani nkhongole / sungankoni ndalama

    Linganizani bwino zinthu kuti mucepetseko nkhongole. Ngati n’kotheka, muzipewa kutenga nkhongole. M’malo mwake muzisungako ndalama kuti mukagulile cimene mufuna.

  • Mwezi uliwonse muzisungako ndalama yocepa yokaseŵenzetsa kutsogolo kapena ya zakugwa mwadzidzidzi.

MUZIGWILA NCHITO MOLIMBIKA KUTI MUKHALITSE PA NCHITO

Baibo imati: “Kugwila nchito iliyonse kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

  • Kalipentala akukhoma msomali.

    Gwilani nchito molimbika / samalani nchito yanu

    Muziiona moyenela nchito yanu. Ngakhale ngati nchito imene mumagwila si imene munali kulakalaka, imakupatsanibe kena kake.

  • Khalani olimbikila nchito komanso odalilika. Izi zingakuthandizeni kuti mukhalitse pa nchito yanu, komanso ngati nchitoyo yatha sicingakhale covuta kupeza ina m’tsogolo.

“Nimagwila nchito iliyonse imene napeza, ngakhale kuti sinaikonde kwenikweni komanso malipilo ake si amene n’nali kuyembekezela. Nthawi zonse nimakhala wodalilika pa nchito, ndipo nimaigwila bwino monga kuti ni nchito yanga.”—Dmitriy.

Ngati mukufunafuna nchito . . .

  • Citam’poni kanthu. Mungatumile foni makampani amene angakhale na nchito imene mungagwile ngakhale kuti sanalengeze kuti afuna kulemba anthu nchito. Dziŵitsani anzanu komanso acibale anu kuti mukusakila nchito.

  • Khalani okonzeka kusintha. N’zosatheka kupeza nchito imene ili na zonse zimene mufuna.

Makolo akukambilana za ndalama pamene ana awo akuseŵela panja.

KUTI MUDZIŴE ZAMBILI, ŵelengani nkhani yakuti: “Zimene Mungacite Ngati Mukupeza Ndalama Zocepa. ”Fufuzani mutu umenewu pa jw.org ku Chichewa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani