LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 4
  • Mmene Anataila Malo Ao Okhalako

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Anataila Malo Ao Okhalako
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Adamu na Hava Sanamvele Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Kuyamba Kwa Umoyo Wovuta
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 4

Nkhani 4

Mmene Anataila Malo Ao Okhalako

ONA zimene zicitika tsopano. Adamu ndi Hava awathamangitsa m’munda wokongola wa Edeni. Udziŵa cimene awathamangitsila?

Cifukwa anacita cinthu coipa kwambili. Conco Yehova wawapatsa cilango. Nanga udziŵa coipa cimene Adamu ndi Hava anacita?

Anacita cinthu cimene Mulungu anawaletsa kuti asacite. Mulungu anawauza kuti ayenela kudya zipatso za mitengo ya m’munda umenewo. Koma anawaletsa kudya zipatso za mtengo umodzi. Anawauza kuti ngati adzadya adzafa. Mulungu anapatula mtengo umenewo kukhala wake-wake. Ndipo tidziŵa kuti n’kulakwa kutenga cinthu ca mwiniwake, si conco? Cabwino, kodi cinacitika n’ciani?

Tsiku lina pamene Hava anali kwa yekha m’munda muja, njoka inayamba kukamba naye. Ganiza cabe njoka kukamba! Inauza Hava kuti adye cipatso ca mtengo umene Mulungu anawaletsa kuti asadye. Koma pamene Yehova anapanga njoka, sanazipange kuti zizikamba iyai. Pamenepa, ndiye kuti panali munthu wina amene anapangitsa kuti njoka imeneyo ikambe. Uganiza munthu ameneyo anali ndani?

Sanali Adamu iyai. Ndiye kuti ayenela kukhala mmodzi wa anthu amene Yehova anapanga kale kwambili akalibe kupanga dziko lapansi. Anthu amenewo ni angelo, ndipo ife sitingawaone. Koma panali mngelo mmodzi amene anakhala wodzitukumula kwambili. Iye anayamba kuganiza kuti anali woyenela kukhala wolamulila monga Mulungu. Ndipo anali kufuna kuti anthu azimvela iye osati Yehova. Mngelo ameneyo ni amene anapangitsa kuti njoka ija ikambe.

Mngelo ameneyo anakwanitsa kupusitsa Hava. Pamene mngelo ameneyo anauza Hava kuti akadya cipatso cimeneco adzakhala monga Mulungu, Hava anakhulupilila. Pamenepo anadya, ndipo Adamu naye anadya. Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu, ndiye cifukwa cake anataya malo ao okongola.

Koma tsiku lina mtsogolo, Mulungu adzapangitsa dziko lonse kukhala labwino monga mmene munda wa Edeni unalili. M’nkhani zakutsogolo, tidzaphunzila mmene ngakhale iwe ungathandizile kupangitsa dziko lapansi kukhala monga munda wokongola. Koma tsopano, tiye tione kuti n’ciani cinacitika kwa Adamu ndi Hava.

Genesis 2:16, 17; 3:1-13, 24; Chivumbulutso 12:9.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani