LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 38
  • Azondi 12

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Azondi 12
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Azondi 12
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yoswa Akhala Mtsogoleli
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mose Amenya Cimwala Ndi Ndodo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Rahabi Abisa Azondi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 38

Nkhani 38

Azondi 12

ONA zipatso zimene anthu awa anyamula. Ona zipatso za mpesa kukula. Zicita kufuna amuna aŵili kuti anyamuzane. Ndipo ona nkhuyu izi ndi makangaza kapena kuti mapamagalaneti. Kodi zipatso zabwino conco zacokela kuti? Zacokela kudziko la Kanani. Ndipo kumbukila kuti Abulahamu, Isaki ndi Yakobo anali kukhala ku Kanani. Koma cifukwa cakuti kunali njala, Yakobo ndi banja lake anasamukila kudziko la Iguputo. Koma apa papita zaka pafupi-fupi 216, ndipo Mose tsopano atsogolela Aisiraeli kubwelela kudziko la Kanani. Iwo afika pamalo ochedwa Kadesi.

Mu dziko la Kanani muli anthu oipa. Mose atuma azondi 12 ndi kuwauza kuti: ‘Mukaone ngati kuli anthu ambili kapena ang’ono, ndipo mukaone ngati ndi anthu amphamvu. Komanso mukaone ngati dziko limenelo lili ndi nthaka yabwino yolimapo zakudya. Mukabweletseko zipatso.’

Pamene azondi abwelako ku Kadesi, auza Mose kuti: ‘Ni dziko labwino kwambili.’ Kuti atsimikize zimene akamba, io aonetsa Mose zipatso zimene abwela nazo. Koma azondi ena 10 akamba kuti: ‘Kuli viŵanthu vikulu-vikulu vamphamvu. Ngati tingayese kulanda dziko lao, vidzatipha.’

Pamene Aisiraeli amvela izi acita mantha kwambili. Ndipo akuti: ‘Cikanakhala bwino kufela ku Iguputo kapena mu cipululu muno. Tidzafa pankhondo, ndipo akazi athu ndi ana athu adzawatenga. Tiyeni tisankhe mtsogoleli wina m’malo mwa Mose, kuti tibwelele ku Iguputo!’

Koma azondi aŵili akhulupilila Yehova, ndipo ayesa kukhazika mitima ya anthu pansi. Maina ao ni Yoswa ndi Kalebe. Iwo akamba kuti: ‘Musaope. Yehova ali nafe. Sitidzavutika kulanda dziko limeneli.’ Koma anthu samvela, cakuti afuna kupha Yoswa ndi Kalebe.

Yehova akalipa kwambili cifukwa ca zimenezi, ndipo auza Mose kuti: ‘Anthu onse azaka kuyambila 20 kukwela m’mwamba sadzaloŵa mu dziko la Kanani. Iwo anaona zozizwitsa zimene ndinacita mu dziko la Iguputo ndi mu cipululu, koma sandikhulupilila. Conco adzazungulila mu cipululu kwa zaka 40, mpaka onse akafe. Yoswa cabe ndi Kalebe ndi amene adzaloŵa mu dziko la Kanani.’

Numeri 13:1-33; 14:1-38

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani