LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 14 nkhani 134-143
  • Zimene Muyenela Kucita Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Muyenela Kucita Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MULUNGU NDI AMENE ANAYAMBITSA MAKONZEDWE A BANJA
  • CITSANZO KWA AMUNA
  • CITSANZO KWA AKAZI
  • CITSANZO CABWINO KWAMBILI KWA MAKOLO
  • CITSANZO KWA ANA
  • CISINSI COPEZELA CIMWEMWE M’BANJA
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe
    Galamuka!—2021
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 14 nkhani 134-143

NKHANI 14

Zimene Muyenela Kucita Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe

  • Kodi muyenela kucita ciani kuti mukhale mwamuna wabwino?

  • Kodi mkazi ayenela kucita ciani kuti asamalile bwino udindo wake?

  • Kodi kukhala kholo labwino kumafuna ciani?

  • Nanga ana angathandize bwanji kuti banja likhale lacimwemwe?

1. Kuti banja likhale lacimwemwe, kodi cisinsi cake n’ciani?

YEHOVA MULUNGU amafuna kuti banja lanu likhale lacimwemwe. Mau ake, Baibo, amapeleka malangizo kwa munthu aliyense m’banja. Amafotokoza mbali imene Mulungu amafuna kuti munthu aliyense m’banja azicita. Pamene aliyense m’banja acita bwino mbali yake, mogwilizana ndi malangizo a Mulungu, zotsatilapo zake zimakhala zabwino kwambili. Yesu anati: “Odala ndi amene akumva mau a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28.

2. Kuti banja likhale lacimwemwe, kodi zimadalila kuzindikila ciani?

2 Ngati tizindikila kuti Yehova ndi amene anayambitsa banja, zimathandiza kwambili kuti banja likhale lacimwemwe. Yehova ameneyu, Yesu anam’chula kuti: “Atate wathu.” (Mateyu 6:9) Cifukwa cakuti Atate wathu wakumwamba ndiye anayambitsa banja, iye amadziŵa bwino zimene zingapangitse mabanja kukhala acimwemwe. (Aefeso 3:14, 15) Conco, kodi Baibo imaphunzitsa ciani za udindo wa aliyense m’banja?

MULUNGU NDI AMENE ANAYAMBITSA MAKONZEDWE A BANJA

3. Kodi Baibo imafotokoza kuti banja linayamba bwanji? Ndipo timadziŵa bwanji kuti zimene imakamba n’zoona?

3 Yehova analenga anthu aŵili oyambilila, Adamu ndi Hava, ndipo anawabweletsa pamodzi kukhala mwamuna ndi mkazi wake. Anawaika m’paladaiso padziko lapansi, m’munda wokongola wa Edeni. Ndiyeno anawauza kuti abeleke ana. Iye anati: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:26-28; 2:18, 21-24) Iyi si nkhani yopeka cabe, kapena nthano iyai. Yesu anaonetsa bwino-bwino kuti zimene buku la Genesis limanena, za mmene banja linayambila, n’zoona. (Mateyu 19:4, 5) Ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambili, ndipo umoyo suli mmene Mulungu anali kufunila, tiyeni tione cimene tikambila kuti n’zotheka kukhala ndi banja lacimwemwe.

4. (a) Kodi aliyense m’banja angathandize bwanji kuti banja lao likhale lacimwemwe? (b) Nanga n’cifukwa ciani kuphunzila za umoyo wa Yesu kuli kofunikila kuti banja likhale lacimwemwe?

4 Aliyense m’banja angathandize kuti banja likhale lacimwemwe ngati atengela citsanzo ca Mulungu mwa kuonetsana cikondi. (Aefeso 5:1, 2) Koma kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Mulungu, popeza sitimamuona? Coyamba, tiyenela kudziŵa mmene Yehova amacitila zinthu. Tingadziŵe zimenezo mwa kuona zocita za mwana wake woyamba amene anam’tumiza padziko lapansi. (Yohane 1:14, 18) Pamene Mwana wa Mulungu ameneyu, Yesu Kristu, anali padziko lapansi, anatengela ndendende Atate wake wakumwamba. Kumvetsela pamene Yesu anali kulankhula, kunali ngati kukhala pamodzi ndi Yehova ndi kumumvetsela pamene akamba. (Yohane 14:9) Conco, mwa kuphunzila za cikondi cimene Yesu anaonetsa ndi kutengela citsanzo cake, aliyense angacite mbali yake kuti banja likhale lacimwemwe.

CITSANZO KWA AMUNA

5, 6. (a) Kodi mmene Yesu anacitila ndi mpingo anapeleka citsanzo canji kwa amuna? (b) Kodi tiyenela kucita ciani kuti Mulungu azitikhululukila macimo?

5 Baibo imakamba kuti amuna ayenela kucita ndi akazi ao monga mmene Yesu anacitila ndi ophunzila ake. Onani malangizo awa a m’Baibo: “Amuna inu, pitilizani kukonda akazi anu monga mmene Kristu anakondela mpingo n’kudzipeleka yekha cifukwa ca mpingowo . . . Mwa njila imeneyi amuna akonde akazi ao monga matupi ao. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda, mmenenso Kristu amacitila ndi mpingo.”—Aefeso 5:23, 25-29.

6 Mmene Yesu anakondela mpingo wa ophunzila ake, anapeleka citsanzo cabwino kwambili kwa amuna. Yesu “anawakonda mpaka pa mapeto,” kupeleka moyo wake kaamba ka io, ngakhale kuti anali opanda ungwilo. (Yohane 13:1; 15:13) Mofananamo, amuna amalimbikitsidwa kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsele mtima.” (Akolose 3:19) Kodi n’ciani cingathandize mwamuna kuseŵenzetsa uphungu umenewu, maka-maka pamene nthawi zina mkazi wake alephela kucita zinthu mozindikila? Ayenela kukumbukila zophophonya zake ndi zimene ayenela kucita kuti akhululukidwe ndi Mulungu. Kodi ayenela kucita ciani? Ayenela kukhululukila ao amene amam’lakwila, kuphatikizapo mkazi wake. Mkazi nayenso ayenela kucita cimodzi-modzi. (Mateyu 6:12, 14, 15) Kodi mwaona cifukwa cimene anthu ena amakambila kuti cikwati cabwino ndi ca anthu aŵili amene amakhululukilana nthawi zonse?

7. Kodi Yesu anali kukumbukila ciani pocita ndi ophunzila ake? Ndipo anapeleka citsanzo canji kwa amuna?

7 Amuna ayenelanso kudziŵa kuti Yesu nthawi zonse anali kuganizila ophunzila ake. Anali kudziŵa zolephela zao ndi zofooka za thupi lao. Mwacitsanzo, pamene io anali otopa, iye anati: “Inuyo bwelani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.” (Maliko 6:30-32) Mofananamo, akazi naonso amafuna kuwaganizila. Baibo imawafotokoza kuti, “ciwiya cosalimba” cimene amuna amalamulidwa kuti azicipatsa “ulemu.” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti onse amuna ndi akazi adzalandila “moyo . . . cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Petulo 3:7) Amuna ayenela kukumbukila kuti cimene cimapangitsa munthu kukhala wofunika kwa Mulungu, si cifukwa cakuti ndi mwamuna kapena mkazi iyai, koma kukhulupilika kwake kwa Mulungu.—Salimo 101:6.

8. (a) Kodi mwamuna amene “amakonda mkazi wake, amadzikonda yekha” bwanji? (b) Kodi kukhala “thupi limodzi” kumatanthauza ciani kwa mwamuna ndi mkazi wake?

8 Baibo imakamba kuti mwamuna amene “amakonda mkazi wake amadzikonda yekha.” Zili conco cifukwa mwamuna ndi mkazi wake “salinso aŵili, koma thupi limodzi,” monga mmene Yesu anakambila. (Mateyu 19:6) Mwa ici, maganizo okhudza za kugonana ayenela kungokhala pakati pa io aŵili cabe. (Miyambo 5:15-21; Aheberi 13:4) Zimenezi zingatheke ngati aliyense aganizila zosoŵa za mnzake mwacikondi, m’malo mongoganizila zake cabe. (1 Akorinto 7:3-5) Tiyenela kukumbukila kuti: “Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” Amuna ayenela kukonda akazi ao monga mmene amadzikondela io eni, pokumbukila kuti adzayankha kwa mutu wao amene ndi Yesu Kristu.—Aefeso 5:29; 1 Akorinto 11:3.

9. Kodi lemba la Afilipi 1:8, limachula khalidwe liti la Yesu? Ndipo n’cifukwa ciani amuna ayenela kuonetsa khalidwe limeneli kwa akazi ao?

9 Mtumwi Paulo anakambapo za “cikondi cacikulu cimene Kristu Yesu ali naco.” (Afilipi 1:8) Cikondi ca Yesu cimeneci cinali cotsitsimula kwa akazi amene anali ophunzila ake. (Yohane 20:1, 11-13, 16) Ndipo akazi naonso amafunitsitsa kuti amuna ao aziwakonda kwambili.

CITSANZO KWA AKAZI

10. Kodi Yesu amapeleka citsanzo canji kwa akazi?

10 Kuti banja liziyenda bwino, limafunikila kukhala ndi mutu. Ndipo ngakhale Yesu nayenso ali ndi mutu umene amaugonjela. Monga mmene ‘mutu wa Kristu ndiye Mulungu, mutu wa mkazi ndi mwamuna.’ (1 Akorinto 11:3) Mmene Yesu amagonjelela umutu wa Mulungu ndi citsanzo cabwino kwambili kwa ife, cifukwa aliyense wa ife ali pansi pa mutu umene ayenela kuugonjela.

11. Kodi mkazi ayenela kuonetsa khalidwe lanji kwa mwamuna wake? Ndipo kucita zimenezi kungakhale kothandiza bwanji?

11 Amuna opanda ungwilo amatha kulakwitsa zinthu, ndipo kaŵili-kaŵili amalephela kucita zonse zofunikila monga mitu ya mabanja. Conco, kodi mkazi ayenela kucita ciani? Iye ayenela kupewa kusuliza zimene mwamuna wake amacita, kapena kuyesa kumulanda umutu. Mkazi angacite bwino kumakumbukila kuti kwa Mulungu, cofunika kwambili ndi mzimu wa mtendele ndi wofatsa. (1 Petulo 3:4) Mwa kuonetsa mzimu umenewo, kudzakhala kotheka kuti mkaziyo azigonjelabe mwamuna wake, ngakhale pamene kungakhale kovuta. Komanso, Baibo imati: “Mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Koma bwanji ngati mwamunayo saona Kristu kukhala Mutu wake? Baibo imalimbikitsa akazi kuti: “Muzigonjela amuna anu kuti ngati ali osamvela mau akopeke, osati ndi mau, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso ao khalidwe lanu loyela ndi ulemu wanu waukulu.”—1 Petulo 3:1, 2.

12. N’cifukwa ciani sikulakwa ngati mkazi akamba maganizo ake mwaulemu?

12 Kaya mwamuna wake ndi wokhulupilila kapena wosakhulupilila, sikuti mkazi amucotsela ulemu ngati mosamala akamba maganizo ake osiyana ndi a mwamuna wake. Maganizo a mkaziyo angakhale abwino kwambili, ndipo banja lonse lingapindule ngati mwamunayo avomeleza maganizo a mkazi wake. Ngakhale kuti Abulahamu sanavomeleze maganizo a mkazi wake Sara pa vuto lina lake la pabanja, Mulungu anamuuza kuti: “Mvela mau ake.” (Genesis 21:9-12) Koma mwamuna akapanga cosankha pankhani ina yake, cimene sicisemphana ndi malamulo a Mulungu, mkazi wake angaonetse kugonjela ngati acilikiza cosankha cimeneco.—Machitidwe 5:29; Aefeso 5:24.

Abraham listening to Sarah

Kodi Sara anapeleka citsanzo cabwino cotani kwa akazi okwatiwa?

13. (a) Kodi lemba la Tito 2:4, 5 limalimbikitsa akazi okwatiwa kucita ciani? (b) Kodi Baibo imakamba ciani pa nkhani ya kupatukana ndi kuthetsa cikwati?

13 Pali zambili zimene mkazi angacite pa udindo wake wosamalila banja. Mwacitsanzo, Baibo imaonetsa kuti akazi okwatiwa ayenela “kukonda amuna ao, kukonda ana ao, kukhala oganiza bwino, oyela, ogwila nchito zapakhomo, abwino ndi ogonjela amuna ao.” (Tito 2:4, 5) Ngati acita bwino udindo wake monga mkazi kapena mai wa ana ake, banja lake lidzayamba kum’konda ndi kum’patsa ulemu nthawi zonse. (Miyambo 31:10, 28) Popeza cikwati ndi mgwilizano wa anthu aŵili opanda ungwilo, mikhalidwe ina yovuta kwambili ingapangitse kuti mwamuna ndi mkazi apatukane kapena kulekana. Baibo imalola kupatukana ngati pali mikhalidwe ina yovuta. Koma kupatukana si nkhani yofunika kuitenga mopepuka, cifukwa Baibo imalangiza kuti: “Mkazi asasiye mwamuna wake, . . . mwamunanso asasiye mkazi wake.” (1 Akorinto 7:10, 11) Conco, cifukwa cokha ca m’Malemba cimene cimalola kuti mwamuna ndi mkazi athetse cikwati ndi pamene mmodzi wa io wacita ciwelewele.—Mateyu 19:9.

CITSANZO CABWINO KWAMBILI KWA MAKOLO

14. Kodi Yesu anali kucita motani ndi ana? Ndipo kodi ana amafunikila ciani kwa makolo ao?

14 Mmene Yesu anali kucitila ndi ana, anapeleka citsanzo cabwino kwambili kwa makolo. Pamene anthu ena anayesa kuletsa ana kuti asafike kwa Yesu, iye anati: “Alekeni ana abwele kwa ine, musawaletse ayi.” Baibo imakamba kuti pamenepo iye “anatenga anao m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuika manja ake pa io.” (Maliko 10:13-16) Ngati Yesu anali kupeza nthawi yoceza ndi ana, kodi inunso simuyenela kucita cimodzi-modzi ndi ana anu? Ana anu safunikila kuceza nao pa tumphindi tocepa cabe, koma nthawi yaikulu. Muyenela kukhala ndi nthawi yowaphunzitsa, cifukwa ndi zimene Yehova amalangiza makolo.—Deuteronomo 6:4-9.

15. Kodi makolo ayenela kucita ciani kuti ateteze ana ao?

15 Pamene dziko likuipila-ipila, ana amafunikila kuti makolo aziwateteza kwa anthu amene angafune kuwavulaza, monga aja amene amanyengelela ana kuti agone nao. Onani mmene Yesu anatetezela ophunzila ake, amene mwacikondi anawacha kuti “ana apamtima.” Pamene adani anam’gwila Yesu, ndipo atatsala pang’ono kufa, iye anati “ngati mukufuna ine, awa alekeni azipita.” (Yohane 13:33; 18:7-9) Inunso monga kholo, muyenela kukhala maso ndi macenjela a Mdyelekezi ofuna kuononga ana anu. Muyenela kuwacenjezelatu.a (1 Petulo 5:8) Masiku ano, ana ali pangozi yaikulu mwa kuuzimu, kuthupi ndi m’makhalidwe kuposa ndi kale lonse.

1. Jesus making time for children; 2. A father discussing the Learn From the Great Teacher book with his son

Kodi makolo angaphunzile ciani poona mmene Yesu anali kucitila ndi ana?

16. Kodi makolo angaphunzilepo ciani poona mmene Yesu anacitila ndi zolakwa za ophunzila ake?

16 Usiku wakuti Yesu adzafa, ophunzila ake anali kutsutsana za amene anali wamkulu pakati pao. M’malo mwakuti Yesu awakalipile, anapitiliza kuwathandiza mwa kukamba nao mwacikondi ndi kuwapatsa citsanzo. (Luka 22:24-27; Yohane 13:3-8) Ngati ndinu kholo, kodi mwaona mmene mungatengele citsanzo ca Yesu pamene muongolela ana anu? Zoona, ana amafunika cilango, koma ciyenela kupelekedwa “pa mlingo woyenela.” (Yeremiya 30:11; Miyambo 12:18) Cilango ciyenela kupelekedwa m’njila yakuti, pambuyo pake, mwana wanu akaone kuti cinali coyenelela.—Aefeso 6:4; Aheberi 12:9-11.

CITSANZO KWA ANA

17. Kodi n’citsanzo cabwino citi cimene Yesu anapeleka kwa ana?

17 Kodi ana naonso pali zimene angaphunzile kwa Yesu? Inde zilipo! Mwa zimene iye mwini anacita, Yesu anaonetsa mmene ana angakhalile omvela kwa makolo ao. Iye anati: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsila.” Ndipo anapitiliza kukamba kuti: “Ndimacita zinthu zom’kondweletsa nthawi zonse.” (Yohane 8:28, 29) Yesu anali womvela kwa Atate wake wakumwamba, ndipo Baibo imauza ana kuti naonso azimvela makolo ao. (Aefeso 6:1-3) Ngakhale kuti Yesu anali mwana wangwilo, anali womvela makolo ake, Mariya ndi Yosefe, amene anali opanda ungwilo. Mosakaikila, kumvela kwa Yesu kunabweletsa cimwemwe cacikulu m’banja mwao.—Luka 2:4, 5, 51, 52.

18. N’cifukwa ciani Yesu anali kumvela Atate wake wakumwamba nthawi zonse? Ndipo ndani amakondwela ngati ana amvela makolo masiku ano?

18 Pa nkhani ya kumvela, kodi ana angatengele bwanji citsanzo ca Yesu kuti akondweletse makolo ao? N’zoona kuti nthawi zina acicepele angaone kuti n’cinthu covuta kumvela makolo ao, koma Mulungu amafuna kuti ana azimvela makolo. (Miyambo 1:8; 6:20) Nthawi zonse Yesu anali kumvela Atate wake wakumwamba, ngakhale pamene zinthu zinali zovuta. Pa nthawi ina, pamene Mulungu anafuna kuti Yesu acite cinthu covuta kwambili, Yesu anakamba kuti: “Ndicotseleni kapu iyi [kutanthauza cinthu cina cake cimene iye anafunikila kucita].” Ngakhale ndi conco, Yesu anacitabe zimene Mulungu anafuna, cifukwa anadziŵa kuti Atate wake anali kudziŵa bwino zimene iye anafunikila kucita panthawiyo. (Luka 22:42) Ana akaphunzila kukhala omvela, amakondweletsa kwambili makolo ao ndi atate wao wakumwamba.b—Miyambo 23:22-25.

A boy resisting the temptation of cigarettes from his peers

Kodi acicepele ayenela kuganizila za ciani akamayesedwa?

19. (a) Kodi Satana amawayesa bwanji ana? (b) Kodi khalidwe loipa la ana lingawakhudze bwanji makolo?

19 Mdyelekezi anayesa Yesu, ndipo sitikaikila kuti amafunanso kuyesa acicepele kuti azicita zinthu zolakwika. (Mateyu 4:1-10) Satana Mdyelekezi amagwilitsila nchito cisonkhezelo ca mabwenzi, cimene cimakhala covuta kwambili kucikana. Conco, n’kofunika kwambili kuti ana azipewa kuyanjana ndi ocita zoipa. (1 Akorinto 15:33) Mwana wa Yakobo, Dina, anali kuceza ndi anthu amene sanali kulambila Yehova, ndipo zimenezi zinacititsa kuti aloŵe m’mavuto ambili. (Genesis 34:1, 2) Ganizani cabe mmene banja lingakhumudwile ngati mwana wina wacita chimo la ciwelewele.—Miyambo 17:21, 25.

CISINSI COPEZELA CIMWEMWE M’BANJA

20. Kuti banja likhale lacimwemwe, kodi aliyense ayenela kucita ciani?

20 Kugwilitsila nchito uphungu wa m’Baibo, kumatithandiza kudziŵa mocitila ndi mavuto a m’banja. Ndipo kugwilitsila nchito uphungu umenewo ndiko cisinsi copezela cimwemwe m’banja. Conco amuna, muzikonda akazi anu, ndipo muzicita nao monga mmene Yesu amacitila ndi mpingo wake. Inunso akazi, muzigonjela amuna anu monga mutu, ndipo muzitengela citsanzo ca mkazi wa pa Miyambo 31:10-31. Makolo, phunzitsani ana anu. (Miyambo 22:6) Atate inu, ‘yang’anilani bwino banja lanu.’ (1 Timoteyo 3:4, 5; 5:8; Akolose 3:20) Ndiponso inu ana, muzimvela makolo anu. Palibe amene ali wangwilo m’banja, aliyense amalakwa. Conco onse m’banja ayenela kukhala odzicepetsa, mwa kupepesana ndi kupemphana cikhululukilo.

21. Kodi ndi zinthu zokondweletsa ziti zimene zili mtsogolo? Ndipo tingakhale bwanji ndi banja lacimwemwe pakali pano?

21 Kunena zoona, Baibo ndi nkhokwe ya uphungu ndi malangizo othandiza pa umoyo wa banja. Imatiphunzitsanso za dziko latsopano la paladaiso limene Mulungu adzabweletsa. M’dziko limenelo, anthu onse adzakhala acimwemwe ndi olambila Yehova. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ha! ati kukondweletsa kwake zinthu zimene atilonjeza mtsogolo. Koma ngakhale pakali pano, tikhoza kukhala ndi banja lacimwemwe mwa kugwilitsila nchito malangizo opezeka m’Mau a Mulungu, Baibo.

a Kuti mudziŵe mmene mungatetezele ana anu, onani mutu 32 m’buku lakuti Phunzilani kwa Mphunzitsi Waluso, lolembedwa ndi Mboni za Yehova.

b Nthawi yokha imene mwana ayenela kukana kumvela makolo m’pamene amuuza kucita cinthu cosemphana ndi malamulo a Mulungu.—Machitidwe 5:29.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Amuna ayenela kukonda akazi ao monga matupi ao.—Aefeso 5:25-29.

  • Akazi ayenela kukonda mabanja ao ndi kulemekeza amuna ao.—Tito 2:4, 5.

  • Makolo ayenela kukonda ana ao, kuwaphunzitsa ndi kuwateteza.—Deuteronomo 6:4-9.

  • Ana ayenela kumvela makolo ao.—Aefeso 6:1-3.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani