LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 10
  • Kodi Kulambila kwa Pabanja n’Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Kulambila kwa Pabanja n’Ciani?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Lambilani Yehova Monga Banja
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Kulambila kwa Pabanja—Zimene Mungacite Kuti Kukhale Kosangalatsa Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kulemekezana m’Banja
    Galamuka!—2024
Onaninso Zina
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 10

PHUNZILO 10

Kodi Kulambila kwa Pabanja n’Ciani?

Banja lisangalala na kulambila kwa pabanja

Ku South Korea

Banja liphunzila Baibo pamodzi

Ku Brazil

Mboni ya Yehova iphunzila Baibo

Ku Australia

Banja likambitsilana nkhani ya m’Baibo

Ku Guinea

Kuyambila kale, Yehova amafuna kuti mabanja onse azipeza nthawi yokhala pamodzi kuti alimbitse uzimu wao ndi ubale wao. (Deuteronomo 6:6, 7) Ndiye cifukwa cake Mboni za Yehova zimapatula nthawi wiki iliyonse yocita kulambila kwa pabanja. Zimakambilana momasuka nkhani za kuuzimu malinga ndi zosoŵa za banja lao. Ngakhale ngati mumakhala nokha, nthawi imeneyi ni mpata wabwino wokhala pansi ndi Mulungu mwa kuphunzila nkhani ya m’Baibo imene mungasankhe.

Ni nthawi yoyandikila kwa Yehova. “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Tikamaphunzila za makhalidwe a Yehova ndi zocita zake kupitila m’Mau ake, timamudziŵa bwino. Njila yosavuta yoyambila kulambila kwa pabanja ndiyo kuŵelengela pamodzi Baibo mokweza kwa mphindi zingapo. Mungacite izi mwa kutsatila ndandanda ya wiki iliyonse ya Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Aliyense m’banja angapatsidwe gao lakuti aŵelenge, ndiyeno pambuyo pake mungakambilane zimene mwaphunzila m’Malemba.

Ni nthawi yolimbitsa mgwilizano pa banja. Mwamuna ndi mkazi, ndiponso makolo ndi ana, amalimbitsa mgwilizano pa banja pamene aphunzilila pamodzi Baibo. Nthawi imeneyi ifunika kukhala yosangalatsa, yamtendele, imene aliyense m’banja amalaka-laka kupezekapo wiki iliyonse. Malinga ndi msinkhu wa ana, makolo angasankhe nkhani zothandiza zimene angakambitsilane, mwina mwa kugwilitsila nchito nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena za pa webusaiti yathu ya jw.org. Mungakambitsilane mavuto amene ana akumana nao kusukulu ndi zimene angacite ndi mavutowo. Kodi simungakonde kuonelelako pulogilamu ya pa JW Broadcasting ndi kukambitsilana mfundo zake pambuyo pake? Mungaphunzile nyimbo zimene mudzaimba pamisonkhano ndipo pambuyo pake mungadyeko twina n’twina.

Nthawi yapadela imeneyi yolambila Yehova pamodzi wiki iliyonse idzathandiza aliyense m’banja kukonda Mau a Mulungu, ndipo iye adzadalitsa kwambili khama lanu.—Salimo 1:1-3.

  • Kodi n’cifukwa ciani timapatula nthawi ya kulambila kwa pabanja?

  • Kodi makolo angacite ciani kuti aliyense m’banja azisangalala ndi kulambila kwa pabanja?

DZIŴANI ZAMBILI

Funsani ena mumpingo kuti afotokoze zimene amacita pa kulambila kwao kwa pabanja. Ndiponso, mungafunse ena kuti akuuzeni mabuku amene alipo pa Nyumba ya Ufumu amene mungagwilitsile nchito pophunzitsa ana anu za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani