Nyimbo 139
Aphunzitseni Kucilimika
Yopulinta
Tikondwa kuphunzitsa anthu
Okonda coonadi.
Onani mmene akulila
M’njila ya coonadi.
(KOLASI)
Yehova, mvelani pempho
Lakuti muwasamale.
Mu dzina la Yesu Khristu
Tipemphela akhale ocilimika.
Tinali kuwapemphelela
M’mavuto awo onse.
Tinali kuwasamalila
Yehova ‘wadalitsa.
(KOLASI)
Yehova, mvelani pempho
Lakuti muwasamale.
Mu dzina la Yesu Khristu
Tipemphela akhale ocilimika.
Akhale odalila M’lungu,
Na Mwana wake Yesu.
Amvele ndipo apilile
Tifuna apambane.
(KOLASI)
Yehova, mvelani pempho
Lakuti muwasamale.
Mu dzina la Yesu Khristu
Tipemphela akhale ocilimika.
(Onaninso Luka 6:48; Mac. 5:42; Afil. 4:1.)