NKHANI 3
Kodi Cifunilo ca Mulungu Kwa Anthu N’ciani?
1. Kodi cifunilo ca Mulungu kwa anthu n’ciani?
MULUNGU ali ndi colinga cabwino kwambili kwa anthu. Iye polenga mwamuna woyamba ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava, anali kufuna kuti akhale m’munda wokongola wa Edeni. Cinali cifunilo ca Mulungu kuti iwo akhale ndi ana, akonze dziko lonse lapansi kukhala paradaiso, ndi kusamalila zinyama.—Genesis 1:28; 2:8, 9, 15; onani Zakumapeto 6.
2. (a) Tidziŵa bwanji kuti Mulungu adzakwanilitsa cifunilo cake? (b) Nanga Baibulo imati ciani za moyo wamuyaya?
2 Muganiza bwanji? Kodi n’zoona kuti ife anthu tidzakhaladi m’paradaiso? Yehova akuti: “Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazicitadi.” (Yesaya 46:9-11; 55:11) Inde, adzakwanilitsa ndithu cifunilo cake, ndipo palibe amene angamuletse. Yehova amatiuza kuti anali ndi colinga polenga dziko lapansi. Iye “sanalilenge popanda colinga.” (Yesaya 45:18) Mulungu amafuna kuti anthu akadzale pa dziko lonse lapansi. Nanga ni anthu abwanji amene Mulungu afuna kuti akakhale m’dziko? Ndipo afuna kuti akakhale kwa utali wanji? Baibulo imakamba kuti: “Olungama [kapena kuti anthu omvela] adzalandila dziko lapansi, Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.
3. Kodi pamabwela funso lanji poona kuti anthu amadwala ndi kufa?
3 Koma lelo lino, anthu amadwala ndi kufa. M’maiko ambili anthu amamenyana ndi kuphana. Kodi ndiye cingakhale cifunilo ca Mulungu cimeneci? Kutali-tali! Conco funso n’lakuti, Nanga zoipa izi zinabwelapo bwanji maka-maka? Baibulo cabe ndiye ingayankhe.
PALI MDANI WA MULUNGU
4, 5. (a) N’ndani anakamba ndi Hava m’munda wa Edeni kupitila mu njoka? (b) N’ciani cimacitika kuti munthu wabwino-bwino akhale kawalala?
4 Baibulo imatiuza kuti Mulungu ali ndi mdani wake. Mdani ameneyo amachedwa “Mdyelekezi ndi Satana.” Satana anaseŵenzetsa njoka pokamba ndi Hava m’munda wa Edeni. (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:1) Anaonetsa ngati kuti njoka ndiyo inali kukamba ndi Hava.—Onani Zakumapeto 7.
5 Ndiye tifunse kuti, Kodi Mulungu ndiye anapanga Satana Mdyelekezi? Iyai. Mngelo wina anadzipanga yekha kukhala Mdyelekezi. Iye anali kumwamba pamene Mulungu anali kulenga dziko lapansi kuti Adamu ndi Hava akhalemo. (Yobu 38:4, 7) Nanga cinacitika n’ciani kuti asinthe? Kuti tipeze yankho, tifunse conco; Kodi munthu amakhala bwanji kawalala? Kodi amabadwa ali kawalala? Iyai, amabadwa wabwino-bwino. Koma vuto limabwela akayamba kukhumbila zinthu za eni ake. Saleka kuganizila zinthu zimenezo, ndipo cilakolako cake cimakula. Ndiye mpata ukapezeka amaba. Ni mmene munthu amakhalila kawalala.—Ŵelengani Yakobo 1:13-15; onani Zakumapeto 8.
6. Kodi mngelo wina anakhala bwanji mdani wa Mulungu?
6 Izi n’zimene zinacitika kwa mngelo amene anakhala Satana. Yehova atalenga Adamu ndi Hava, anawauza kuti akhale ndi ana ndi ‘kudzaza dziko lapansi.’ (Genesis 1:27, 28) Mngelo uja ayenela anaganiza kuti: ‘Anthu onse amene adzabadwa akhoza kudzakhala olambila ine m’malo molambila Yehova.’ Cifukwa anapitiliza kuganizilapo, maganizo amenewo anakula mwa iye. Mngelo ameneyu anafunitsitsa kuti anthu azilambila iye. Cotulukapo, ananama Hava ndi kumusoceletsa. (Ŵelengani Genesis 3:1-5.) Mwa ici, anakhala Satana Mdyelekezi, mdani wa Mulungu.
7. (a) Adamu ndi Hava anafa cifukwa ciani? (b) Nanga ife, n’cifukwa ciani timakalamba ndi kufa?
7 Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu, conco anadya cipatso coletsedwa. (Genesis 2:17; 3:6) Kumeneko kunali kucimwila Yehova. Ndipo monga mwa mau a Mulungu, iwo anafa m’kupita kwa nthawi. (Genesis 3:17-19) Ana a Adamu ndi Hava anabadwa ndi ucimo, conco iwonso anafa. (Ŵelengani Aroma 5:12.) Kuti timvetsetse cifukwa cake ana nawonso anakhala ocimwa, tiyeni tiganizile citsanzo ici: Tikambe kuti mwatenga cikombole cothifuka (olo cobenda), ndi kuyamba kuumba nchelwa, kapena kupanga mabuloko. Kodi nchelwa kapena mabuloko amene angatuluke m’cikombole cimeneco adzakhala owongoka bwino-bwino? N’zosatheka! Onse adzakhala othifuka kapena obenda. N’cimodzi-modzi ndi ife anthu. Pamene Adamu anapandukila Mulungu, anakhala wocimwa. Ndiye popeza ndife ana ake, tonse ndife ocimwa, kapena kuti “obenda.” Conco cifukwa ndife ocimwa, timakalamba ndi kufa.—Aroma 3:23; onani Zakumapeto 9.
8, 9. (a) Kodi Satana anali kufuna kuti Adamu ndi Hava akhulupilile ciani? (b) N’cifukwa ciani Mulungu sanawaphe apanduwo pa nthawi imene ija?
8 Pamene Satana anapangitsa Adamu ndi Hava kucimwila Mulungu, anayambitsa cipani copandukila ulamulilo wa Yehova. Anafuna kuti Adamu ndi Hava akhulupilile kuti Yehova ni wabodza, ndipo ni wolamulila woipa amene sanali kuwafunila zabwino. M’ceni-ceni, Satana anali kukamba kuti anthu safunikila Mulungu kuwauza zocita. Kutanthauza kuti Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wosankha okha cabwino ndi coipa. Kodi Yehova akanacita ciani? Akanafuna, sembe anawapha apandu onsewo ndi kufafaniza cipani cawo copandukila olamulilo. Koma kodi izi zikanaonetsa kuti Satana ni wabodza? Iyai.
9 Ndiye cifukwa cake Yehova sanaphe apandu aja pa nthawi imeneyo. Analola nthawi yakuti anthu adzilamulile okha. Ndiyo inali njila yabwino yoonetsa poyela kuti Satana ni wabodza, ndi kuti Yehova amafunila anthu zabwino zokha-zokha. Tidzaphunzila zambili m’Nkhani 11. Kodi inu muona bwanji pa zimene Adamu ndi Hava anasankha kucita? Kodi cinali cinthu canzelu kukhulupilila Satana ndi kupandukila Mulungu? Tangoganizani! Zonse zimene anali nazo anawapatsa ni Yehova. Anawapatsa moyo wangwilo, malo okongola okhalamo, ndi nchito yokondweletsa. Koma Satana sanawacitilepo cabwino ciliconse. Mukanakhala inu, sembe munacita bwanji?
10. Kodi aliyense wa ife afunika kupanga cosankha canji?
10 Lelo lino, aliyense wa ife afunika kupanga cosankha. Ndipo moyo wathu udalila cosankha cimeneco. Tikhoza kusankha kumvela Yehova monga Wolamulila wathu, ndi kum’thandiza kutsimikizila Satana kuti ni wabodza. Kapena tikhoza kusankha Satana kukhala wolamulila wathu. (Salimo 73:28; ŵelengani Miyambo 27:11.) Koma ni anthu ocepa cabe amene amamvela Mulungu. Ndi iko komwe, Mulungu sindiye alamulila dziko lino. Lomba ngati sindiye alamulila dziko, ndiye kuti amene alamulila dziko n’ndani?
N’NDANI ALAMULILA DZIKO?
Sembe maufumu a pa dziko sanali a Satana, kodi akanalonjeza kuwapatsa kwa Yesu?
11, 12. (a) Satana anafuna kupatsa Yesu maufumu onse. Kodi tiphunzilapo ciani? (b) Ni malemba ati aonetsa kuti Satana ndiye alamulila dziko?
11 Yesu anali kum’dziŵa amene alamulila dziko. Pa nthawi ina, Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a pa dziko ndi ulemelelo wawo.” Ndiyeno Satana analonjeza Yesu kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi mutangogwada pansi n’kundiwelamila kamodzi kokha.” (Mateyu 4:8, 9; Luka 4:5, 6) Lomba dzifunseni kuti, ‘Sembe maufumu amenewo sanali ake Satana, kodi akanalonjeza kumupatsa Yesu?’ Kutali-tali! Conco mfundo ni yakuti, maboma onse ali m’manja mwa Satana.
12 Mwina mungadabwe kuti: ‘Satana angakhale bwanji wolamulila dziko? Kodi Yehova Mulungu Wamphamvuyonse, sindiye analenga zinthu zonse?’ (Chivumbulutso 4:11) Zoona, Mulungu ndiye Mlengi. Ngakhale n’conco, Yesu anakamba kuti “wolamulila wa dzikoli” ni Satana. (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Ngakhale mtumwi Paulo anati Satana Mdyelekezi ndiye “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akorinto 4:3, 4 ) Mtumwi Yohane nayenso analemba kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.
KODI DZIKO LA SATANA LIDZAWONONGEDWA BWANJI?
13. N’cifukwa ciani dziko latsopano lifunika?
13 Dziko lino lingoipilako-ipilako. Nkhondo, ciwawa, ziphuphu ndi cinyengo (kolapushoni) zili paliponse. Mulimonse mmene angayesele, anthu sangakwanitse kutsiliza mavuto amenewa. Koma Mulungu adzawononga dziko loipa ili pa nkhondo ya Aramagedo, ndi kubweletsa dziko latsopano la cilungamo.—Chivumbulutso 16:14-16; onani Zakumapeto 10.
14. Kodi Mulungu anasankha ndani kukhala Mfumu mu Ufumu wake? Nanga Baibulo inakambilatu ciani za Yesu?
14 Yehova anasankha Yesu Khiristu kukhala Mfumu m’boma lake la kumwamba, kapena kuti mu Ufumu wa Mulungu. Zaka zambili-mbili zapitazo, Baibulo inalosela kuti Yesu adzalamulila monga “Kalonga Wamtendele,” ndipo ulamulilo wake sudzatha. (Yesaya 9:6, 7) Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphelela boma limeneli kuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mu Nkhani 8, tidzaphunzila mmene Ufumu wa Mulungu udzacotselapo maboma onse ali pa dziko pano. (Ŵelengani Danieli 2:44.) Pambuyo pake, Ufumuwo udzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso.—Onani Zakumapeto 11.
DZIKO LATSOPANO LILI PAFUPI
15. Kodi “dziko lapansi latsopano” n’ciani?
15 Baibulo imalonjeza kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela,” ndipo “mmenemo mudzakhala cilungamo.” (2 Petulo 3:13; Yesaya 65:17) M’Baibulo, mau akuti “dziko lapansi” nthawi zina amatanthauza anthu amene akhala pa dziko lapansi. (Genesis 11:1) Conco, “dziko lapansi latsopano” lolungama ni anthu onse amene amamvela Mulungu ndi kudalitsidwa ndi iye.
16. Ni mphatso yanji imene Mulungu adzapatsa anthu amene adzakhala m’dziko latsopano? Nanga tiyenela kucita ciani kuti tikalandileko mphatso imeneyo?
16 Yesu analonjeza kuti anthu amene adzakhala m’dziko latsopano adzalandila “moyo wosatha.” (Maliko 10:30) Kodi tifunika kucita ciani kuti tikalandileko mphatso imeneyi? Yankho tilipeza pa Yohane 3:16 ndi Yohane 17:3. (Ŵelengani.) Lomba tiyeni tione mmene umoyo udzakhalila m’Paradaiso pa dziko lapansi, malinga ndi kunena kwa Baibulo.
17, 18. Tidziŵa bwanji kuti mtendele udzakhala kulikonse padziko lapansi, ndi kuti tidzakhala osungika?
17 Nkhondo, upandu, ciwawa, ndi zoipa zonse zidzatha. Pa dziko lapansi sipadzatsala munthu woipa ngakhale mmodzi. (Salimo 37:10, 11) Mulungu ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’ (Salimo 46:9; Yesaya 2:4) Pa dziko lapansi padzakhala cabe anthu okonda Mulungu ndi omumvela. Mtendele udzakhalapo kwamuyaya.—Salimo 72:7.
18 Anthu a Yehova adzamva kukhala osungika. Kale, Aisiraeli omvela Mulungu anali kukhala osungika cifukwa Mulungu anali kuwacinjiliza. (Levitiko 25:18, 19) M’Paradaiso, sitidzaopa ciliconse kapena munthu aliyense. Tidzakhala ocinjilizika nthawi zonse.—Ŵelengani Yesaya 32:18; Mika 4:4.
19. Titsimikiza bwanji kuti m’dziko latsopano mudzakhala cakudya ca mwana alilenji?
19 Padzakhala cakudya ca mwana alilenji. Baibulo imati: “Pa dziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.” (Salimo 72:16) Yehova ‘Mulungu wathu adzatidalitsa,’ ndipo “dziko lapansi lidzapeleka zipatso zake.”—Salimo 67:6.
20. Tidziŵa bwanji kuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso?
20 Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Anthu adzakhala ndi nyumba zocititsa kaso ndi malo okongola. (Ŵelengani Yesaya 65:21-24; Chivumbulutso 11:18.) Dziko lonse lidzakhala lokongola mmene munda wa Edeni unalili. Yehova adzatipatsa zonse zofunikila. Baibulo imati za Mulungu: “Mumatambasula dzanja lanu ndi kukhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.”—Salimo 145:16.
21. Tidziŵa bwanji kuti anthu adzakhala pa mtendele ndi nyama?
21 Anthu adzakhala pa mtendele ndi nyama. Nyama sizidzavulazanso anthu. Ana ang’ono sadzaopa ciliconse, ngakhale nyama zoopsa zimene timaopa masiku ano.—Ŵelengani Yesaya 11:6-9; 65:25.
22. Kodi Yesu adzacita ciani kwa anthu odwala?
22 Sipadzapezeka wodwala. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anacilitsa anthu ambili. (Mateyu 9:35; Maliko 1:40-42; Yohane 5:5-9) Koma monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzacilitsa anthu onse. Palibe adzakamba kuti: ‘Ine nidwala.’—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
23. Kodi Mulungu adzacita ciani kwa anthu amene anamwalila?
23 Akufa adzauka. Mulungu analonjeza kuti adzaukitsa akufa mamiliyoni ambili, ndi kuti iwo akhoza kudzakhala ndi moyo wamuyaya. Baibulo imati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Ŵelengani Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
24. Mumvela bwanji mukaganizila zokhala m’Paradaiso?
24 Conco, kusankha ni kwathu. Kaya tidzasankha kuphunzila za Yehova ndi kum’tumikila, kapena tidzasankha kumangocita zimene mtima wathu ufuna, zili kwa ife. Koma tikasankha kutumikila Yehova, tidzakhala ndi tsogolo labwino. Mwamuna wina ali pafupi kufa, anapempha Yesu kuti akamukumbukile. Yesu poyankha anamulonjeza kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Mu Nkhani yotsatila tidzaphunzila za Yesu Khiristu, ndi mmene adzakwanilitsila malonjezo okondweletsa a Yehova.