NKHANI 18
Kodi N’dzipeleke Kwa Mulungu Kuti N’kabatizike?
1. Kodi mungaganizile za ciani pamene mwaphunzila buku ino?
M’BUKU ino, mwaphunzila zinthu zambili za coonadi ca m’Baibulo. Mwaphunzila za lonjezo la Mulungu la moyo wosatha, mkhalidwe wa anthu akufa, ndi ciyembekezo cakuti akufa adzauka. (Mlaliki 9:5; Luka 23:43; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Mwina munayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova, ndipo mumakhulupilila kuti cipembedzo cawo ni coona. (Yohane 13:35) Kapenanso ubwenzi wanu ndi Yehova wayamba kukhala wolimba, ndipo mufuna kumutumikila. Conco mungadzifunse kuti: ‘Niyenela kucita ciani kuti nitumikile Mulungu?’
2. N’cifukwa ciani munthu wa ku Itiyopiya anafuna kubatizika?
2 Zimenezo n’zimene munthu wina wa ku Itiyopiya anaganiza m’nthawi ya Yesu. Pa nthawi inayake Yesu ataukitsidwa, wophunzila wake Filipo analalikila kwa munthu ameneyo. Filipo anakhutilitsa munthuyo kuti Yesu anali Mesiya. Munthu wa ku Itiyopiyayo anakhudzidwa mtima kwambili ndi zimene anaphunzila, cakuti nthawi imeneyo anati: “Taonani! Si awa madzi ambili. Cikundiletsa kubatizidwa n’ciani?”—Machitidwe 8:26-36
3. (a) Kodi Yesu anapeleka lamulo lanji kwa otsatila ake? (b) Nanga munthu ayenela kubatizika bwanji?
3 Baibulo imaphunzitsa kuti ngati munthu afuna kutumikila Yehova, ayenela kubatizika. Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti: ‘Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga, ndipo muziwabatiza.’ (Mateyu 28:19) Yesu anapeleka citsanzo mwa kubatizika iye mwini. Pa ubatizo wake, anam’miza [kaya kum’mbiza] thupi lonse, osati kumuwaza cabe madzi pa mutu iyai. (Mateyu 3:16) Ngakhale masiku ano, Mkhiristu aliyense pobatizika afunika kumumbiza thupi lonse m’madzi.
4. Kodi ubatizo wanu umaonetsa ciani kwa ena?
4 Mukabatizika, mumaonetsa anthu ena kuti mufuna kukhala bwenzi la Mulungu ndi kumutumikila. (Salimo 40:7, 8) Conco, mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi niyenela kucita ciani kuti nibatizike?’
CIDZIŴITSO NDI CIKHULUPILILO N’ZOFUNIKA
5. (a) Kuti mubatizike, mufunika kucita ciani coyamba? (b) N’cifukwa ciani misonkhano ya Cikhiristu ni yofunika kwambili?
5 Mukalibe kubatizika, coyamba mufunika kudziŵa Yehova ndi Yesu. Munayamba kale kucita zimenezi mwa kuphunzila Baibulo. (Ŵelengani Yohane 17:3.) Koma kuphunzila cabe si kokwanila. Baibulo imakamba kuti muyenela ‘kudziŵa molongosoka’ cifunilo ca Yehova. (Akolose 1:9) Kupezeka ku misonkhano ya Mboni za Yehova kudzakuthandizani kukhala pa unansi wolimba ndi Yehova. Ndiye cifukwa cake mufunika kumapezeka ku misonkhano yonse.—Aheberi 10:24, 25.
Musanabatizike, mufunika kuphunzila Baibulo
6. Kodi muyenela kuphunzila zinthu zoculuka bwanji musanabatizike?
6 Koma Yehova sayembekezela kuti mudziŵe zonse za m’Baibulo kuti mubatizike iyai. Ngakhale munthu wa ku Itiyopiya uja, sanafunikile kucita kudziŵa zonse kuti abatizike. (Machitidwe 8:30, 31) Ndipo tonse tidzapitiliza kuphunzila za Mulungu kwamuyaya. (Mlaliki 3:11) Koma kuti mubatizike, mufunika kuphunzila ndi kuvomeleza ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo.—Aheberi 5:12.
7. Kodi kuphunzila Baibulo kwakuthandizani bwanji?
7 Baibulo imakamba kuti: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Conco mukalibe kubatizika, coyamba mufunika kukhala ndi cikhulupililo. Baibulo imatiuza kuti anthu ena ku Korinto wamakedzana, ‘anayamba kukhulupilila ndi kubatizika’ atamva zimene otsatila a Yesu anali kuphunzitsa. (Machitidwe 18:8) Ngakhale inu, kuphunzila Baibulo kwakuthandizani kukhala ndi cikhulupililo m’malonjezo a Mulungu. Mukhulupililanso kuti nsembe ya Yesu ili ndi mphamvu imene ingatipulumutse ku ucimo ndi imfa.—Yoswa 23:14; Machitidwe 4:12; 2 Timoteyo 3:16, 17.
MUZIUZAKO ENA COONADI CA M’BAIBULO
8. N’ciani cingakulimbikitseni kuuzako ena zimene mumaphunzila?
8 Pamene muphunzila zambili m’Baibulo, ndi kuona mmene yakuthandizilani mu umoyo wanu, cikhulupililo canu cidzalimbilako-limbilako. Ndipo mudzakhala ofunitsitsa kuuzako ena zimene muphunzila. (Yeremiya 20:9; 2 Akorinto 4:13) Koma n’ndani amene mungauuzeko zimene muphunzila?
Cikhulupililo ciyenela kukulimbikitsani kuuzako ena zimene mumakhulupilila
9, 10. (a) Kodi mungayambile kwa ndani kuwauzako zimene mumaphunzila? (b) Nanga muyenela kucita ciani kuti muyambe kulalikila ndi mpingo?
9 Mungacite bwino kumauzako ena zimene mumaphunzila, monga abululu ŵanu, anzanu, aneba anu, ndi amene mumagwila nawo nchito. Koma muyenela kucita zimenezi mokoma mtima ndi mwacikondi. M’kupita kwa nthawi, mudzayamba kulalikila pamodzi ndi mpingo. Pamene mudzaonela kuti ndinu wokonzeka, mungauze wa Mboni amene amaphunzila nanu Baibulo. Ndiyeno, amene muphunzila naye Baibulo akaona kuti ndinu wokonzeka bwino, ndipo umoyo wanu ni wogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo, akulu aŵili a mpingo adzakumana ndi inu aŵili.
10 N’ciani cimene akuluwo adzakambilana nanu? Adzafuna kuona ngati mumamvetsetsa ndi kukhulupilila ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo. Adzafunanso kuona ngati mumatsatila mu umoyo wanu zimene Baibulo imaphunzitsa. Adzafunanso kutsimikiza ngati ndinu wofunitsitsadi kukhala Mboni ya Yehova. Simuyenela kucita mantha kukamba ndi akulu cifukwa iwo amayang’anila anthu onse mu mpingo, kuphatikizapo inu. (Machitidwe 20:28; 1 Petulo 5:2, 3) Pambuyo pokumana ndi akulu aŵili, adzakuuzani ngati ndinu oyenelela kuyamba kulalikila ndi mpingo.
11. N’cifukwa ciani n’kofunika kukonza bwino umoyo wanu mukalibe kuyamba kulalikila pamodzi ndi mpingo?
11 Mwina akulu angakuuzeni kuti muyembekezele pang’ono kuti muyambe mwakonza mbali zina mu umoyo wanu, mukalibe kuyamba kulalikila pamodzi ndi mpingo. N’cifukwa ciani n’kofunika kwambili kuti muyambe mwakonza mbali zimenewo za umoyo wanu? Cifukwa pamene tilalikila kwa ena, timaimilako Yehova Mulungu. Conco, umoyo wathu uyenela kukhala wolemekeza Mulungu.—1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21.
LAPANI NDI KUTEMBENUKA
12. N’cifukwa ciani anthu onse afunika kulapa?
12 Palinso cinthu cina cimene muyenela kucita mukalibe kubatizika. Mtumwi Petulo anakamba kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe.” (Machitidwe 3:19) Kodi kulapa kumatanthauza ciani? Kumatanthauza kumvela cisoni kwambili pa macimo onse amene mwakhala mukucita. Mwacitsanzo, ngati munali kucita zaciwelewele, mufunika kulapa. Ngakhale ngati muona kuti mu umoyo wanu wonse simunacitepo macimo alionse, mufunikilabe kulapa cifukwa tonse timacimwa ndipo tifunika kupempha Mulungu kuti atikhululukile.—Aroma 3:23; 5:1.
13. Kodi “kutembenuka” kumatanthauza ciani?
13 Kodi kumvela cisoni cifukwa ca macimo amene munali kucita n’kokwanila? Iyai. Petulo ananenanso kuti mufunikila “kutembenuka.” Kutanthauza ciani? Kutanthauza kulekelatu khalidwe yoipa iliyonse imene munali kucita ndi kuyamba kucita zabwino. Tiyeni tiyelekeze kuti muyenda ku malo acilendo. Pambuyo poyenda mtunda utali, mwaona kuti njila imene mwatenga ni yolakwika. Kodi mungacite ciani? Mungayambe kuyenda pang’ono-pang’ono, kuima, kutembenuka, ndi kutenga njila yoyenelela. N’cimodzi-modzi ndi kuphunzila Baibulo. Mudzazindikila kuti pali zinthu zina mu umoyo wanu zimene mudzafunika kusintha. Khalani wofunitsitsa “kutembenuka,” kutanthauza kusintha zinthu zimenezo, ndi kuyamba kucita zoyenela.
MUFUNIKANSO KUDZIPELEKA
Kodi munam’lonjeza kale Yehova kuti mufuna kumutumikila?
14. Kodi munthu amadzipeleka bwanji kwa Mulungu?
14 Sitepu ina yofunika kupanga mukalibe kubatizika ni kudzipeleka kwa Yehova. Podzipeleka kwa Yehova, mumalonjeza Yehova m’pemphelo kuti mudzalambila iye yekha cabe, ndi kuti kucita cifunilo cake ndiye cidzakhala cinthu cacikulu mu umoyo wanu.—Deuteronomo 6:15.
15, 16. N’ciani cimalimbikitsa munthu kuti adzipeleke kwa Mulungu?
15 Kucita cipangano cotumikila Yehova yekha kwa umoyo wanu wonse, kuli monga cipangano ca cikwati ndi munthu amene mumakonda ndi mtima wanu wonse. Tiyelekezele kuti mwamuna wayamba kuyendela mbeta. Pamene mwamuna aona makhalidwe abwino a mkaziyo, cikondi cake pa iye cimakulilako-kulilako, mpaka amatsimikiza mtima za kumanga naye banja. Ngakhale kuti kumanga banja si nkhani ya maseŵela, mwamuna amalimba mtima kuti adzatenga udindo umenewo cifukwa wamukonda mkaziyo ndi mtima wonse.
16 Ngakhale inu, pamene mupitiliza kuphunzila za Yehova, cikondi canu pa iye cidzakulilako-kulilako, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kum’tumikila. Cimeneci cidzakulimbikitsani kuti mupeleke pemphelo lomulonjeza kuti mufuna kum’tumikila. Baibulo imakamba kuti aliyense wofuna kutsatila Yesu ayenela ‘kudzikana yekha.’ (Maliko 8:34) Nanga kudzikana ndiye kucita ciani? Kumatanthauza kuti kumvela Yehova ndiye cinthu cimene mumaika patsogolo mu umoyo wanu. Ndiye kuti cifunilo ca Yehova cimakhala cinthu cofunika kupambana zofuna zanu kapena zolinga zanu zilizonse.—Ŵelengani 1 Petulo 4:2.
MUSADZIKAIKILE
17. N’cifukwa ciani anthu ena sadzipeleka kwa Yehova?
17 Anthu ena amaopa kudzipeleka kwa Yehova cifukwa coganiza kuti angaphwanye cipangano cawo. Amawopa kukhumudwitsa Yehova. Ndipo amaona kuti kusadzipeleka kuliko bwino, cifukwa akacimwa Yehova sangawaimbe mlandu.
18. N’ciani cingakuthandizeni kucotsa mantha akuti mungakhumudwitse Yehova?
18 Ngati mumakonda Yehova simudzazengeleza kudzipeleka cifukwa coopa kuti tsiku lina mungamucimwile. Cifukwa comukonda ndi mtima wonse, mudzakhala wofunitsitsa kusunga cipangano canu ndi iye. (Mlaliki 5:4; Akolose 1:10) Simudzaona kuti kusunga malamulo a Yehova n’kovuta. Mtumwi Yohane anakamba kuti: ‘Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo ake ndi osalemetsa.’—1 Yohane 5:3.
19. N’cifukwa ciani simuyenela kuopa kudzipeleka kwa Yehova?
19 Simufunikila kucita kukhala wangwilo kuti mudzipeleke kwa Yehova. Iye sayembekezela kuti tizicita zimene sitingakwanitse. (Salimo 103:14) Iye adzakuthandizani kucita zinthu zoyenela. (Yesaya 41:10) Dalilani Yehova ndi mtima wanu wonse, ndipo ‘iye adzaongola njila zanu.’—Miyambo 3:5, 6.
KULENGEZA POYELA CIKHULUPILILO CANU
20. Pamene mudzadzipeleka kwa Mulungu, sitepu yotsatila idzakhala ciani?
20 Kodi ndinu wokonzeka kudzipeleka kwa Yehova? Pamene mudzadzipeleka kwa Yehova, mudzakhala wokonzeka kupanga sitepu yotsatila, kubatizika.
21, 22. Kodi mungalengeze bwanji poyela za cikhulupililo canu?
21 Mukadzipeleka kwa Yehova, mudzafunika kudziŵitsa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu wa mpingo wanu kuti munadzipeleka kwa Yehova ndipo mufuna kubatizika. Iye adzapempha akulu ena kuti akakambilane nanu mafunso okhudza ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo. Ngati akuluwo avomelezana kuti ndinu woyenelela kubatizika, adzakuuzani kuti mudzabatizika pa msonkhano wa cigawo kapena wa dela wotsatila. Pa msonkhano umenewo padzakambidwa nkhani yofotokoza tanthauzo la ubatizo. Ndiyeno wokamba nkhaniyo adzafunsa opita ku ubatizo mafunso aŵili osavuta. Mwa kuyankha mafunso amenewo ‘mudzalengeza poyela’ za cikhulupililo canu.—Aroma 10:10.
22 Ndiyeno pambuyo pake mudzabatizika. Adzakumbizani thupi lonse m’madzi. Ubatizo wanu udzakhala umboni kwa anthu wakuti munadzipeleka kwa Yehova, ndipo lomba ndinu wa Mboni za Yehova.
CIMENE UBATIZO WANU UMATANTHAUZA
23. Kodi kubatizika “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela” kumatanthauza ciani?
23 Yesu anakamba kuti ophunzila ake adzabatizika “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela.” (Ŵelengani Mateyu 28:19.) Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Zimatanthauza kuti mumazindikila ulamulilo wa Yehova ndi udindo wa Yesu pa kukwanilitsa colinga ca Mulungu. Mumazindikilanso mmene Mulungu amagwilitsila nchito mzimu wake woyela kukwanilitsa cifunilo cake.—Salimo 83:18; Mateyu 28:18; Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 1:21.
Pamene mudzabatizika, mudzaonetsa kuti mufuna kucita cifunilo ca Mulungu
24, 25. (a) Kodi ubatizo umatanthauza ciani? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsilizila?
24 Ubatizo umatanthauza cinthu cina cofunika kwambili. Munthu akambizidwa m’madzi, cimatanthauza kuti wafa ku umoyo wake wakale, kapena kuti kulekelatu makhalidwe ake akale. Pamene avuuka m’madzi, cimatanthauza kuuka ku umoyo watsopano wocita cifunilo ca Mulungu. Kucokela pa ubatizo, munthu lomba amayamba kutumikila Yehova kwa umoyo wake wonse. Ayenela kukumbukila kuti anadzipeleka kwa Yehova, osati kwa munthu, ku gulu, kapena ku nchito iyai.
25 Mukadzipeleka kwa Mulungu, ubwenzi wanu ndi iye udzalimba kwambili. (Salimo 25:14) Ici sicitanthauza kuti munthu adzapulumuka cabe cifukwa cakuti anabatizika, iyai. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitilizani kukonza cipulumutso canu, mwamantha ndi kunjenjemela.” (Afilipi 2:12) Ubatizo ni poyambila cabe. Nanga mungacite ciani kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ukhale wamuyaya? Nkhani yotsilizila m’buku ino idzafotokoza zimene muyenela kucita.