LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 8 tsa. 26-tsa. 27
  • Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Abulahamu—mnzake Wa Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yehova Anamucha kuti “Bwenzi Langa”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Mulungu Ayesa Cikhulupililo Ca Abulahamu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Mukuyembekezela “Mzinda Wokhala Ndi Maziko Eni-eni”?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 8 tsa. 26-tsa. 27
Abulahamu na Sara alonga katundu wawo, na kucoka mu mzinda wa Uri

PHUNZILO 8

Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu

Cakufupi na mzinda wa Babele, panali mzinda wina wochedwa Uri. Anthu a mu mzindawu anali kulambila milungu ina yambili osati Yehova. Koma munali munthu wina amene anali kulambila Yehova yekha. Dzina lake anali Abulahamu.

Yehova anauza Abulahamu kuti: ‘Siya nyumba yako ndi abale ako. Upite kudziko limene ndidzakusonyeza.’ Ndiyeno Mulungu anamulonjeza kuti: ‘Iwe udzakhala mtundu waukulu, ndipo anthu ambili pa dziko lapansi ndidzawacitila zabwino cifukwa ca iwe.’

Abulahamu sanadziŵe kumene Yehova anamuuza kuti apite. Koma anadalila Yehova na mtima wonse. Conco, Abulahamu, mkazi wake Sara, atate ake a Tera, komanso Loti mwana wa m’bale wake, analonga katundu wawo wonse na kuyamba ulendo wautali.

Abulahamu anali na zaka 75 pamene anakafika na banja lake ku dziko limene Yehova anafuna kuwaonetsa. Linali dziko la Kanani. Ali kumeneko, Mulungu analonjeza Abulahamu kuti: ‘Ndidzapeleka dziko ili kwa ana ako.’ Koma pa nthawiyi, Abulahamu na Sara anali okalamba, ndipo analibe mwana aliyense. Nanga Yehova anakakwanilitsa bwanji lonjezo lake?

Abulahamu na banja lake paulendo wopita kudziko la Kanani

“Mwa cikhulupililo, Abulahamu . . . anamvela ndi kupita kumalo amene anali kuyembekezela kuwalandila monga colowa. Iye anapitadi, ngakhale sanadziŵe kumene anali kupita.”—Aheberi 11:8

Mafunso: Kodi Yehova anauza Abulahamu kucita ciani? Nanga n’ciani cimene Yehova analonjeza Abulahamu?

Genesis 11:29–12:9; Machitidwe 7:2-4; Agalatiya 3:6; Aheberi 11:8

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani