LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 13 tsa. 36-tsa. 37 pala. 1
  • Yakobo na Esau Akhalanso Pamtendele

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yakobo na Esau Akhalanso Pamtendele
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Ana Amapasa Osiyana
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yakobo Analandila Coloŵa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 13 tsa. 36-tsa. 37 pala. 1
Yakobo agwada pansi ndipo Esau amuthamangila

PHUNZILO 13

Yakobo na Esau Akhalanso pa Mtendele

Yehova analonjeza Yakobo kuti adzamuteteza, monga mmene anatetezela Abulahamu na Isaki. Yakobo anakhazikika ku malo ochedwa Harana. Kumeneko anakwatila na kukhala na banja lalikulu, ndipo analemela ngako.

Patapita nthawi, Yehova anauza Yakobo kuti: ‘Bwelela kudziko lakwanu.’ Conco, Yakobo na banja lake anayamba ulendo wautali wobwelela kwawo. Ali m’njila, atumiki ake anabwela kwa Yakobo na kumuuza kuti: ‘M’bale wanu Esau akubwela, ndipo ali na amuna 400!’ Yakobo anacita mantha kuti Esau afuna kumucita coipa pamodzi na banja lake. Anapemphela kwa Yehova kuti: ‘Conde, nipulumutseni kwa m’bale wanga.’ Tsiku lotsatila, Yakobo anatumizila Esau nkhosa zambili, mbuzi, ng’ombe, ngamila, komanso abulu monga mphatso.

Yakobo ali yekha-yekha usikuwo, anaona mngelo! Mngeloyo anayamba kulimbana naye. Anagwebana mpaka m’mawa. Olo kuti Yakobo anavulala, analimbikilabe. Lomba mngelo anati: ‘Nileke nizipita.’ Koma Yakobo anati: ‘Sinikulekani, mpaka coyamba munidalitse.’

Potsilizila pake, mngeloyo anadalitsa Yakobo. Lomba Yakobo anadziŵa kuti Yehova sadzalola Esau kuti amuvulaze.

M’maŵa mwake, Yakobo anaona Esau na amuna 400 akubwela capatali. Yakobo anapita kutsogolo kwa banja lake, na kukagwada pamaso pa m’bale wake maulendo 7. Esau anathamangila Yakobo na kumukumbatila. Amphundu aŵiliwo anagwetsa misozi kwambili, ndipo anakhalanso pa mtendele. Uganiza Yehova anamvela bwanji na mmene Yakobo anacitila zinthu pa nkhaniyi?

Esau anabwelela ku nyumba kwake, nayenso Yakobo anapitiliza na ulendo wake. Yakobo anali na ana 12 aamuna. Maina awo anali Rubeni, Simiyoni, Levi, Yuda, Dani, Nafitali, Gadi, Aseri, Isakara, Zebuloni, Yosefe, na Benjamini. Mmodzi wa ana ake, Yosefe, Yehova anam’gwilitsila nchito kupulumutsa anthu Ake. Udziŵa mmene anacitila zimenezi? Tidzaona m’nkhani yotsatila.

“Pitilizani kukonda adani anu ndi kupemphelela amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:44, 45

Mafunso: Tidziŵa bwanji kuti Yakobo anali kufunitsitsa kulandila dalitso? Nanga anacita ciani kuti akhalenso pa mtendele na m’bale wake?

Genesis 28:13-15; 31:3, 17, 18; 32:1-29; 33:1-18; 35:23-26

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani