PHUNZILO 24
Sanasunge Lonjezo
Yehova anauza Mose kuti: ‘Kwela m’phili muno ubwele kwa ine. Nidzalemba malamulo anga pa miyala yosema na kukupatsa.’ Mose anakwela m’phili, ndipo anakhala mmenemo kwa masiku 40 usana na usiku. Mose ali m’philimo, Yehova analemba Malamulo 10 pa miyala iŵili yosema na kum’patsa.
Patapita nthawi, Aisiraeli anaganiza kuti Mose anawathaŵa. Conco, anauza Aroni kuti: ‘Tifuna munthu wina wakuti atitsogolele. Tipangile mulungu!’ Aroni anati: ‘Nipatseni golide wanu.’ Iye anasungunula golideyo na kupanga fano la mwana wa ng’ombe. Lomba anthuwo anati: ‘Mwana wa ng’ombe uyu ndiye Mulungu wathu amene anatitulutsa mu Iguputo!’ Anayamba kulambila fano limenelo na kucita cikondwelelo. Kodi izi zinali zolakwika? Inde, cifukwa anthuwo analonjeza kuti adzalambila Yehova yekha cabe. Koma apa lomba anaphwanya lonjezo lawo.
Yehova anaona zimene zinali kucitika. Cotelo anauza Mose kuti: ‘Seluka, pita kuli anthuwo. Iwo sakunimvela ndipo akulambila mulungu wonyenga.’ Mose anaseluka m’philimo atanyamula miyala iŵili yosema.
Atafika pafupi na msasa, anamvela anthu akuimba. Ndiyeno, anaona kuti anthuwo akuvina na kugwadila fano la mwana wa ng’ombe lija. Mose anakwiya kwambili. Pamenepo anaponyela pansi miyala iŵili ija ndipo inaphwanyika. Kenako anaphwanya fano limenelo. Ndiyeno anafunsa Aroni kuti: ‘Kodi anthu awa akunyengelela bwanji kuti ucite cinthu coipa kwambili ici?’ Aroni anati: ‘Musakalipe. Imwe mudziŵa bwino mmene anthu aŵa alili. Iwo anali kufuna mulungu. Conco, n’nasungunula golide wawo pa moto na kupanga mwana wa ng’ombe ameneyu.’ Aroni sanafunikile kucita zimenezo. Pamenepo Mose anabwelela m’phili, kukacondelela Yehova kuti awakhululukile anthuwo.
Yehova anakhululukila aja amene anamumvela na mtima wonse. Kodi waona kuti Aisiraeli anacita bwino kumvelela Mose mtsogoleli wawo?
“Ukalonjeza kwa Mulungu usamacedwe kukwanilitsa lonjezo lako, cifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa. Uzikwanilitsa zinthu zimene walonjeza.”—Mlaliki 5:4