LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 27 tsa. 68-tsa. 69 pala. 2
  • Anapandukila Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anapandukila Yehova
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Ndodo Ya Aroni Imela Maluŵa
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 27 tsa. 68-tsa. 69 pala. 2
Kora na anzake aimilila pamaso pa Mose na Aroni

PHUNZILO 27

Anapandukila Yehova

Pa nthawi ina Aisiraeli akali m’cipululu, Kora, Datani, Abiramu, ndi anthu ena 250 anaukila Mose. Anamuuza kuti: ‘Talema nawe lomba! Iwe ungakhale bwanji mtsogoleli wathu? Naye Aroni angakhale bwanji mkulu wa ansembe? Sikuti Yehova ali na iwe na Aroni cabe, alinso na ise tonse.’ Yehova sanakondwele nazo zimenezi. Anaona kuti kuukila Mose, kunali kum’pandukila Yehova!

Mose anauza Kora na anzake kuti: ‘Maŵa mukabwele ku cihema na zofukizila zanu zodzala nsembe zofukiza. Yehova adzationetsa amene iye adzasankha.’

M’maŵa mwake, Kora na amuna 250 anayenda kukakumana na Mose ku cihema. Kumeneko iwo anayamba kufukiza nsembe olo kuti sanali ansembe. Ndiyeno Yehova anauza Mose na Aroni kuti: ‘Cokani pakati pa Kora na anzake.’

Kora ndiye anapita kukaonana na Mose ku cihema. Koma Datani, Abiramu, na mabanja awo anakana kuyendako. Yehova anauza Aisiraeli kuti acoke ku misasa ya Kora, Datani, na Abiramu. Nthawi yomweyo Aisiraeli anacokako. Datani, Abiramu, na mabanja awo anaimilila panja pa matenti awo. Basi mwadzidzidzi, nthaka inang’ambika n’kuwameza onse! Ku cihema kuja, Kora na anzake 250 ananyeka na moto wocokela kumwamba.

Nthaka ing’ambika pakati na kumeza Datani, Abiramu, komanso mabanja awo

Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Tenga ndodo ya mtsogoleli wa fuko lililonse na kulembapo dzina la mtsogoleliyo. Koma pa ndodo ya fuko la Levi, ulembepo dzina la Aroni. Uike ndodo zimenezo mkati mwa cihema colambililako. Ndodo ya munthu amene nasankha idzamela maluŵa.’

Tsiku lokonkhapo, Mose anatenga ndodo zonse na kuzibweletsa kwa atsogoleli a mafuko. Ndodo ya Aroni ndiye inamela maluŵa, ndipo inali na zipatso za maamondi zakupsa. Izi zinatsimikizila kuti Yehova anali atasankha Aroni kukhala mkulu wa ansembe.

“Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela.”—Aheberi 13:17

Mafunso: N’cifukwa ciani Kora na anzake anaukila Mose? Tidziŵa bwanji kuti Yehova anasankha Aroni kukhala mkulu wa ansembe?

Numeri 16:1–17:13; 26:9-11; Salimo 106:16-18

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani