PHUNZILO 56
Yosiya Anali Kukonda Cilamulo ca Mulungu
Yosiya anakhala mfumu ya Yuda pamene anali na zaka 8 cabe. M’masiku amenewo, anthu anali kucita zamatsenga na kulambila mafano. Yosiya atafika zaka 16, analimbikila kuphunzila mmene angalambilile Yehova m’njila yoyenela. Atafika zaka 20, anayamba kuwononga mafano na maguwa ansembe m’dziko lawo. Ndipo pamene anafika zaka 26, analinganiza zakuti kacisi wa Yehova akonzedwe.
Hilikiya mkulu wansembe, anapeza mpukutu wa Cilamulo ca Yehova m’kacisi. Mwina mpukutuwo ni umene uja unalembewa na Mose. Kalembela wa mfumu, Safani, anabweletsa mpukutuwo kwa Yosiya na kuyamba kumuŵelengela mokweza. Pamene Yosiya anali kumvetsela, anazindikila kuti kwa zaka zambili anthu akhala akuphwanya malamulo a Yehova. Conco anauza Hilikiya kuti: ‘Yehova watikwiila kwambili. Pitani mukakambe naye. Adzatiuza zimene tiyenela kucita.’ Yehova anayankha kupitila mwa mneneli wamkazi Hulida. Iye anati: ‘Ayuda asiya kutsatila malamulo anga. Conco nidzawalanga, koma osati pamene Yosiya akulamulila monga mfumu, cifukwa iye waonetsa kudzicepetsa.’
Mfumu Yosiya atamva uthengawu, anapita kukacisi na kusonkhanitsa Ayuda onse. Ndiyeno anaŵelengela anthu onsewo mokweza Cilamulo ca Yehova. Yosiya pamodzi ndi anthu onse analonjeza kuti adzamvela Yehova na mtima wawo wonse.
Kwa zaka zambili, Ayuda sanali kucita cikondwelelo ca Pasika. Koma Yosiya ataŵelenga m’Cilamulo, anapeza kuti cikondwelelo ca Pasika cifunika kucitika caka ciliconse. Ndiyeno anauza anthuwo kuti: ‘Tidzacitila Yehova cikondwelelo ca Pasika.’ Kenako Yosiya anakonzekela kupeleka nsembe zambili. Anakonzanso gulu lokaimba pakacisi. Anthu anacita cikondwelelo ca Pasika. Pambuyo pake anacita cikondwelelo ca mikate yopanda cofufumitsa kwa masiku 7. Kucokela m’masiku a Samueli, sipanacitikepo cikondwelelo ca Pasika monga cimeneci. Yosiya anali kukondadi Cilamulo ca Mulungu. Kodi iwe umakonda kuphunzila za Yehova?
“Mawu anu ndi nyale younikila kumapazi anga, ndi kuwala kounikila njila yanga.” —Salimo 119:105