Mawu Oyamba a Cigawo 7
Cigawo cino cifotokoza mbili ya Mfumu Sauli na Mfumu Davide, pa zaka pafupi-fupi 80. Poyamba, Sauli anali wodzicepetsa komanso woopa Mulungu, koma m’kupita kwa nthawi anasintha na kuleka kukonkha malangizo a Yehova. Ndipo Yehova anamukana. M’kupita kwa nthawi, iye anauza Samueli kudzoza Davide kuti akhale mfumu ya Aisiraeli. Cifukwa ca nsanje, Sauli anayesa kangapo konse kuti aphe Davide, koma Davide sanabwezele. Mwana wa Sauli, Yonatani, anadziŵa kuti Davide anasankhiwa na Yehova. Conco anali wokhulupilika kwa Davide. Olo kuti Davide anacita macimo aakulu, sanakane uphungu wa Yehova. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa kufunika kocilikiza makonzedwe a Mulungu nthawi zonse.