NYIMBO 75
‘Ine Nilipo, N’tumizeni!’
Yopulinta
(Yesaya 6:8)
1. Anthu anyoza Mulungu
Aipitsa dzina lake.
Zoipa zikacitika
M’lungu ndiye wacititsa.
Ndani adzaŵathandiza,
Kudziŵa kuti si M’lungu?
(KOLASI 1)
“Ine M’lungu nitumeni,
Nitamande dzina lanu.
Ine nilipo n’tumizeni
Yehova nitumeni.”
2. Ena sayopa Mulungu
Amalambila mafano.
Ndipo ena alambila
Mafumu a dziko lawo.
Ndani adzaŵacenjeza,
Za nkhondo ya M’lungu wathu?
(KOLASI 2)
“Ine M’lungu nitumeni,
nikaŵacenjeze onse.
Ine nilipo n’tumizeni
Yehova nitumeni.”
3. ‘Ofatsa adandaula
Zoipa zaonjezeka.
Na mtima wofunitsitsa
Asakila coonadi.
Ndani adzaŵathandiza,
Kuti apeze co’nadi?
(KOLASI 3)
“Ine M’lungu nitumeni,
Kuti nikaŵathandize.
Ine nilipo n’tumizeni
Yehova nitumeni.”
(Onaninso Sal. 10:4; Ezek. 9:4.)