NYIMBO 92
Malo a Dzina Lanu
Yopulinta
(1 Mbiri 29:16)
1. O Yehova, ni mwayi wathu,
Kukumangilani nyumba!
Ise pano tiipeleka,
Kwa inu Mulungu wathu.
Zilizonse tingapeleke
Inde n’zanu kale zonse.
Mphamvu, maluso, cuma cathu,
Mokondwa tikupatsani.
(KOLASI)
Tipeleka malo aya,
Conde alandileni.
Achukitse dzina lanu
Inde mutamandike.
2. Pamalo ano tiloleni
Tikutamandeni M’lungu.
Tidzasamalila nyumbayi,
Tidziŵa kuti ni yanu.
Ikhale umboni kwa onse,
Wakuti ‘se ndise anu.
Ulemelelo wa nyumbayi,
Inde, ukwele kwa inu.
(KOLASI)
Tipeleka malo aya,
Conde alandileni.
Achukitse dzina lanu
Inde mutamandike.
(Onaninso 1 Maf. 8:18, 27; 1 Mbiri 29:11-14; Mac. 20:24.)