NYIMBO 117
Ubwino
Yopulinta
(2 Mbiri 6:41)
1. O Yehova M’lungu wathu,
Ise mwatidalitsa.
Ndinu wokhulupilika
Wabwino m’zinthu zonse.
Mwationetsa cifundo
Cifukwa mutikonda.
Tidzakutumikilani
Nakukulambilani.
2. Tiona ubwino wanu
Mwa anthu munasankha.
Amalengeza uthenga
Na kucita zabwino.
Mwa akulu a mumpingo,
Tipita patsogolo.
Tipatseni mzimu wanu
Tionetse ubwino.
3. Kwa abale athu onse,
Tionetse ubwino.
Tipempha mutithandize
Kukonda athu onse.
Ku mipingo na mabanja,
Ndi kwa anansi athu,
Tipempha thandizo lanu,
Tionetse ubwino.
(Onaninso Sal. 103:10; Maliko 10:18; Agal. 5:22; Aef. 5:9.)