LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • CO-pgm17 masa. 7-8
  • Mau kwa Osonkhana

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mau kwa Osonkhana
  • Pulogilamu ya Msonkhano Wacigawo wa mu 2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAMITING’I APADELA
  • SUKULU YA ALENGEZI A UFUMU Apainiya a zaka zapakati pa 23 na 65 amene afuna kuwonjezela utumiki wawo, apemphedwa kukapezeka pamiting’i ya Sukulu ya Alengezi a Ufumu, patsiku lacitatu la msonkhano uno. Tidzalengeza malo na nthawi pasadakhale. MAU KWA OSONKHANA
  • Mau kwa Osonkhana
    Pulogilamu ya Msonkhano Wacigawo wa mu 2018
  • Mawu kwa Osonkhana
    Pulogilamu ya Msonkhano Wacigawo wa mu 2019
  • Mawu kwa Osonkhana
    Pulogilamu ya Msonkhano Wacigawo wa mu 2020
  • Mawu kwa Osonkhana
    Pulogilamu ya Msonkhano Wacigawo wa mu 2024
Onaninso Zina
Pulogilamu ya Msonkhano Wacigawo wa mu 2017
CO-pgm17 masa. 7-8

Mau kwa Osonkhana

MAMITING’I APADELA

UTUMIKI WA PA BETELI Ofalitsa obatizika a zaka 35 kubwela pansi, ndipo afuna utumiki wa pa Beteli, akapezeke pamiting’i ya utumiki wa pa Beteli patsiku loyamba la msonkhano uno kumasana. Tidzalengeza malo na nthawi pasadakhale.

SUKULU YA ALENGEZI A UFUMU Apainiya a zaka zapakati pa 23 na 65 amene afuna kuwonjezela utumiki wawo, apemphedwa kukapezeka pamiting’i ya Sukulu ya Alengezi a Ufumu, patsiku lacitatu la msonkhano uno. Tidzalengeza malo na nthawi pasadakhale. MAU KWA OSONKHANA

AKALINDE Akalinde alipo kuti akutumikileni. Conde, gwilizanani nawo mwa kutsatila malangizo awo okhudza koika mamotoka, kutsogolela anthu, kusungilatu malo okhala, na nkhani zina.

UBATIZO Opita ku ubatizo ayenela kukhala pamalo amene awasungila kutsogolo kwa pulatifomu, kupatulapo ngati pakonzedwa malo ena. Ayenela kutelo ikalibe kuyamba nkhani ya ubatizo patsiku laciŵili kum’maŵa. Aliyense ayenela kubweletsa thaulo na covala caulemu coloŵa naco m’madzi.

ZOPELEKA Pamaloŵa ndalama zambili kuti pakhale malo okhalapo okwanila, zolankhulila, na zinthu zina zothandiza kuti msonkhano ukhale wosangalatsa, nakuti utithandize kuyandikila Yehova. Ndalama zimenezo zimacokela pa zopeleka zanu zaufulu, ndipo zimathandizanso panchito yathu ya padziko lonse. Kuti zisakuvuteni kucita copeleka, mudzaona mabokosi olembewa mooneka bwino amene aikidwa pamalo osiyana-siyana pamsonkhano pano. Timaonga zikomo ngako pa zopeleka zanu zonse. Bungwe Lolamulila liyamikila kwambili pa kuwolowa manja kwanu kocilikiza zinthu za Ufumu.

CITHANDIZO CA ODWALA Conde, kumbukilani kuti Dipatimenti ya Cithandizo ca Odwala ni ya ZAKUGWA MWADZIDZIDZI CABE.

CIPINDA CA ZOTAIKA Zinthu zonse zopezeka ziyenela kupelekedwa ku Dipatimenti ya Zotaika. Ngati mwataya ciliconse, pitani ku dipatimenti imeneyi ndi kuwauza cimene mwataya. Ana amene asoŵa makolo awo, nawonso ayenela kupelekedwa ku dipatimenti imeneyi. Komabe, dziŵani kuti dipatimenti imeneyi si kosungitsila ana iyai. Conde samalilani ana anu, ndipo khalani nawo pamodzi.

MALO OKHALA Conde, ganizilani anzanu. Kumbukilani kuti, mungasungile cabe malo okhala anthu amene mudzayenda nawo pamodzi, amene mukhala nawo nyumba imodzi, kapena amene mumaphunzila nawo Baibo. Conde, ngati simusungila wina malo, musaike zinthu pamalo amene ena afunika kukhalapo.

NCHITO YODZIPELEKA Ngati mufuna kuthandizako nchito pamsonkhano uno, pitani ku Dipatimenti ya Nchito Yodzipeleka, ndipo adzakuuzani zofunika kucita.

Wokonzedwa na Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani