LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 24
  • Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kudziŵa Bwino Za Angelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Zolengedwa Zauzimu Zimatikhudza Bwanji?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tsutsani Mdyelekezi ndi Zocita Zake Zacinyengo
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Kukaniza Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 24
Phunzilo 24. Cifanizilo ca mngelo.

PHUNZILO 24

Kodi Angelo Ndani Kwenikweni Ndipo Amacita Ciyani?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Yehova amafuna kuti tidziŵe za banja lake la kumwamba. Banja limenelo ni la angelo, ochedwa “ana a Mulungu.” (Yobu 38:7) Kodi Baibo imakamba ciyani za angelo? Kodi iwo amacita ciyani? Ndipo kodi angelo onse ali m’banja la Mulungu?

1. Kodi Angelo Ndani?

Yehova anayamba walenga angelo asanapange dziko lapansi. Mofanana na Mulungu, iwo ni anthu auzimu osaoneka okhala kumwamba. (Aheberi 1:14) Angelowo ali mamiliyoni ambili-mbili kumwambako, ndipo aliyense ni wosiyana na mnzake. (Chivumbulutso 5:11) Iwo amacita “zimene Yehova wanena mwa kumvela malamulo ake.” (Salimo 103:20) M’nthawi zamakedzana, Yehova nthawi zina anali kutumiza angelo ake kukapeleka mauthenga kwa anthu ake, kapena kukawathandiza, kapenanso kukawapulumutsa. Masiku ano, angelo amatsogolela Akhristu kwa anthu ofuna kuphunzila za Mulungu.

2. Kodi Satana na ziŵanda zake ndani?

Angelo ena anamupandukila Yehova. Mngelo woyamba kupanduka anali “iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Satana anali kufuna ulamulilo, conco ananyengelela anthu aŵili oyambawo, komanso angelo ena, kuti agwilizane naye pa kupandukila Mulungu. Angelo amene anapanduka amenewo amachedwa ziŵanda. Yehova anawapitikitsa kumwamba n’kuwagwetsela padziko lapansi, ndipo pothela pake adzawawonongelatu.—Ŵelengani Chivumbulutso 12:9, 12.

3. Kodi Satana na Ziŵanda zake amayesa bwanji kutisoceletsa?

Satana na ziŵanda zake amasoceletsa anthu ambili kupitila mu zamizimu, zimene ni mcitidwe woipa woyesa kukambilana na mizimu. Mwacitsanzo, anthu ena amafunsila kwa openda nyenyezi, olosela zam’tsogolo, owombeza, komanso kwa asing’anga. Ena amafuna cithandizo ca mankhwala coloŵetsapo zamizimu. Ndiponso anthu amanamizidwa kuti akhoza kukambilana na anthu amene anafa. Koma Yehova amaticenjeza kuti: “Musatembenukile kwa olankhula ndi mizimu ndipo musafunsile olosela zam’tsogolo.” (Levitiko 19:31) Amatipatsa cenjezo limeneli pofuna kutiteteza kwa Satana na ziŵanda zake. Iwo ni adani a Mulungu, ndipo amafuna kuticita zoipa.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phuzilani zinthu zabwino zimene angelo amacita, kuopsa kwa zamizimu, na mmene tingadzitetezele kwa Satana na ziŵanda zake.

Mngelo akutsogolela Mboni za Yehova ziŵili mu ulaliki wa nkhomo na nkhomo.

4. Angelo amathandiza anthu kuphunzila za Yehova

Angelo a Mulungu salalikila mwacindunji kwa anthu. M’malo mwake, amatsogolela alambili a Mulungu kwa anthu ofuna kuphunzila za iye. Ŵelengani Chivumbulutso 14:6, 7, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani tifunikila thandizo la angelo polalikila?

  • Kodi zimakulimbikitsani kudziŵa kuti angelo akhoza kukutsogolelani kwa anthu ofuna kumva za m’Baibo? Cifukwa ciyani?

Zinthu zamizimu zimaphatikizapo thabwa la zamizimu, galasi lobulungila lamatsenga, buku la zipuku, njuga zamaula, tuzidoli twamatsenga, zofuzikiza, zithumwa, komanso mankhwala acambu.

5. Pewani zamizimu

Satana na ziŵanda zake ni adani a Yehova. Iwo alinso adani kwa ife. Ŵelengani Luka 9:38-42, na kukambilana funso ili:

  • Kodi ziŵanda zimacita ciyani kwa anthu?

Tisadziitanile tokha ziŵanda mu umoyo wathu. Ŵelengani Deuteronomo 18:10-12, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi ziŵanda zimayesa kutikopa na kukambilana nafe m’njila ziti? Nanga kwanuko anthu amakonda kulankhula na ziŵanda m’njila ziti?

  • Kodi inu mukuona kuti n’cinthu cabwino kuti Yehova amaletsa kucitako zamizimu? Cifukwa ciyani?

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

VIDIYO: “Tsutsani Mdyelekezi” (5:02)

  • Kodi mukuona kuti cithumwa cimene Palesa anaveka mwana wake padzanja ndico cinabweletsa vutolo? Cifukwa ciyani?

  • Kodi Palesa anayenela kucita ciyani kuti onse atetezeke ku ziŵanda?

Akhristu enieni nthawi zonse akhala akuzitsutsa ziŵanda. Ŵelengani Machitidwe 19:19, komanso 1 Akorinto 10:21, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani muyenela kuwononga cinthu ciliconse cokhudza zamizimu?

Mzimayi akuwononga zinthu zosiyana-siyana zamatsenga pozitentha m’moto.

6. Pambanani nkhondo yolimbana na Satana komanso ziŵanda zake

Satana ndiye amalamulila ziŵanda. Koma angelo okhulupilika amatsogoleledwa na mngelo wamkulu Mikayeli, dzina lina la Yesu. Kodi Mikayeli ali na mphamvu zoculuka bwanji? Ŵelengani Chivumbulutso 12:7-9, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi amene ali na mphamvu zambili ndani, Mikayeli na angelo ake, kapena Satana na ziŵanda zake?

  • Kodi muganiza otsatila a Yesu ayenela kumuopa Satana na ziŵanda zake?

Mukhoza kupambana nkhondo yolimbana na Satana na ziŵanda zake. Ŵelengani Yakobo 4:7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mungadziteteze bwanji kwa Satana na ziŵanda zake?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Palibe vuto kucitako maseŵelo a zamizimu, kapena kutamba mafilimu ake. Zangokhala zosangalatsa cabe.”

  • N’cifukwa ciyani maganizo amenewa ni olakwika?

CIDULE CAKE

Angelo okhulupilika amatithandiza. Koma Satana na ziŵanda zake ni adani a Yehova, ndipo iwo amaseŵezetsa zamizimu kusoceletsa anthu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi angelo a Yehova amathandiza bwanji anthu kuphunzila za iye?

  • Kodi Satana na ziŵanda zake ndani?

  • N’cifukwa ciyani muyenela kutalikilana nazo zamizimu?

Colinga

FUFUZANI

Onani umboni woonetsa kuti Yesu ndiye mngelo wamkulu, Mikayeli.

“Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani umboni wotsimikizila kuti Mdyelekezi si maganizo cabe oipa mumtima mwa munthu.

“Kodi Mdyerekezi Alipodi?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani mmene mayi wina anamasukila ku ziŵanda.

“Anapeza Chifuno cha Moyo” (Nsanja ya Olonda, July 1, 1993)

Onani mmene Satana amaseŵenzetsela zamizimu popusitsa anthu.

“Kudziŵa Zoona pa Nkhani ya Matsenga ndi Ufiti” (Njila ya Kumoyo Wamuyaya, Kodi Mwaipeza?, mbali 5)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani