LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 2
  • Kukamba Mwacibadwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukamba Mwacibadwa
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Filipo Anacitila Zimenezi
  • Tiphunzilaponji kwa Filipo?
  • Tengelani Citsanzo ca Filipo
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano ndi Colinga Cakuti Ticite Ulaliki Wamwai
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Kodi Muwathetse Makambilano?
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 2

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Mlaliki Filipo akukambilana na mwamuna wa ku Itiyopiya yemwe akuŵelenga mpukutu atakhala m’galeta.

Machitidwe 8:30, 31

PHUNZILO 2

Kukamba Mwacibadwa

Mfundo Yaikulu: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili!”—Miy. 15:23.

Mmene Filipo Anacitila Zimenezi

Mlaliki Filipo akukambilana na mwamuna wa ku Itiyopiya yemwe akuŵelenga mpukutu atakhala m’galeta.

VIDIYO: Filipo Alalikila Nduna ya ku Itiyopiya

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 8:30, 31. Kenaka, ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi Filipo anayambitsa motani makambilano?

  2. N’cifukwa ninji tingati imeneyi inali njila yacibadwa yoyambila makambilano na munthu, kenaka n’kum’phunzitsa mfundo yatsopano ya coonadi?

Tiphunzilaponji kwa Filipo?

2. Ngati tilankhula mwacibadwa, munthuyo adzakhala womasuka, komanso adzamvetsela uthenga wathu mosavuta.

Tengelani Citsanzo ca Filipo

3. Khalani oyang’anitsitsa. Nkhope ya munthu, manja ake, ngakhale thupi lake, zingatiuze zambili za munthuyo. Kodi aoneka na cidwi cofuna kuceza nanu? Mungayambe nkhani ya m’Baibo mongom’funsa kuti, “Kodi mudziŵa kuti . . . ?” Pewani kuumiliza munthu woonekelatu kuti safuna kukambilana naye.

4. Khalani woleza mtima. Musaumilizike kungoyamba na mfundo ya m’Baibo. Yembekezani mpata woyenela kuti muiloŵetsepo mosavutikila. Mwinanso mpatawo ungadzapezeke bwino pa ulendo wina wodzaceza naye.

5. Khalani wokonzeka kusintha. N’kutheka makambilano anu angaloŵele kwina kumene simunayembekezele. Zikatelo, kambilanani naye mfundo ina imene angagwilizane nayo, na kusiya imene munaikonzekela.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mlal. 3:1, 7; 1 Akor. 9:22; 2 Akor. 2:17; Akol. 4:6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani